Loading...
Larger font
Smaller font
Copy
Print
Contents
 • Results
 • Related
 • Featured
No results found for: "".
 • Weighted Relevancy
 • Content Sequence
 • Relevancy
 • Earliest First
 • Latest First
  Larger font
  Smaller font
  Copy
  Print
  Contents

  MUTU 5—KUDZIPEREKA

  LONJEZANO la Mulungu liri lakuti, “Ndipo mudzandifuna Ine, ndi kundipeza, pamene mundifuna ndi mtima wanu wonse.” (Yer. 29: 13. )MOK 31.1

  Mtima wonse udziperekedwa kwa Mulungu, titapanda kutero, kusintha sikungacitike mwa ife kumene kungatibwezere m’cifaniziro cace. Mwa cibadwidwe ife tinalekana ndi Mulungu. Mzimu Woyera ufotokoza makhalidwe athu ndi mau otere: “Akufa ndi zolakwa ndi zocimwa zanu;” “Mutu wonse uli kudwala, ndi mtima wonse walefuka;” “m’menemo mulibe cangwiro.” Ife tagwidwa mu msampha wa Satana; “M’menemo anagwidwa naye, ku cifuniro cace.” (Aefeso 2: 1; Yesaya 1: 5, 6; 2 Tim. 2: 26. ) Mulungu afuna kuticiritsa ndi kutimasula ife. Koma popeza izi zifunika kusandulika kweni kweni, kukonzanso mkhalidwe wathu wonse, tiyenera kudzipereka athunthu kwa Iye.MOK 31.2

  Nkhondo yomenyana ndi cifuniro cathu ndiyo nkhondo yaikuru koposa zonse, Kudzipereka tokha, kupereka zonse ku cifuniro ca Mulungu, pafunika nkhondo; koma moyo udzigonjera Mulungu usanakonzedwe kukhala woyera.MOK 31.3

  Ufumu wa Mulungu, si wonga umene angauonetsere Satana, wokhazikika pa cigonjero ca khungu, ndi kulamulira kosayenera. Umadandaulira kwa anzeru ndi a cikumbumtima. “Tiyeni tsono, tiweruzane.” (Yesaya 1: 18), ndiko kuitana kwa Mlengi kwa anthu amene adawapanga. Mulungu sakakamiza cifuniro ca olengedwa ace. Iye sangathe kulandira cipembedzo cimene sicicokera mu mtima wofuna ndi wolola. Cigonjero cokakamiza cidzaletsa kukula kweni kweni kwa mtima kapena makhalidwe; cidzangomcititsa munthu ngati makina. Cimeneci siciri cifuniro ca Mlengi. Iye afuna kuti munthu, amene ali nchito yacifumu ya mphamvu yace ya kulenga, adzakule kwambiri monga angakhoze. Iye atiikira patsogolo pathu msinkhu wa dalitso umene afuna kuti tiufikire mwa cisomo cace. Iye atiitana ife kuti tidzipereke kwa Iye, kuti acite cifuniro cace mwa ife. Zatsalira ife kuti tisankhe ngati tifuna kumasulidwa ku ukapolo wa zoipa, ndi kudzagawana nawo ufulu wa ulemerero wa ana a Mulungu.MOK 31.4

  Pakudzipereka tokha kwa Mulungu, tiyenera kucotsa zonse zimene zingatilekanitse ndi Iye. Cifukwa cace Mpulumutsi ati, “Cifukwa cace yense wa inu amene sakaniza zonse ali nazo sakhoza kukhala wophunzira wanga.” (Luka 14: 33. ) Ciri conse ca kukoka mtima kuucotsa kwa Mulungu ciyenera kusiyidwa. Cuma ndilo fano la anthu ambiri. Cikondi ca pa ndalama, cilakolako ca cuma, ndiwo unyolo wa golidi umene umawamangirira kwa Satana. Anthu ena amapembedza kumveka ndi ulemu wa dziko lapansi. Fano la ena ndilo kufuna mtendere wa iwo okha ndi kupewa katundu wawo. Koma nsinga za ukapolozi ziyenera kudulidWa. Sitingathe kudzigawa pakati kukhala theka lina kwa Ambuye ndi theka lina ku dziko lapansi. Sitingathe kukhala ana a Mulungu ngati sitidzipereka athunthu kwa Iye. Alipo anthu amene amadziyesera kuti ali kutumikira Mulungu, pamene ali kukhulupirira mphamvu zawo kumvera malamulo a Mulungu, kupanga okha makhalidwe abwino, ndi kupeza cipulumutso. Mitima yawo sigundidwa ndi nzeru zakuya za cikondi ca Kristu, koma afuna kugwira nchito za Cikristu, monga ngati kuti Mulungu amawauza kuti adzalowa kumwamba ndi nchito zawozo. Cipembedzo cotere ciri cacabe. Pamene Kristu akhala mu mtima, moyo udzadzazidwa ndi cikondi cace, ndi cimwemwe ca kulankhula naye, kotero kuti udzaumirira kwa Iye; ndipo pa kuganizira za Iye, udzaiwala za kudzikonda wekha. Kukonda Kristu ndiko kudzakhale kasupe wa nchito zako. Iwo amene amva cikondi cokakamiza ca Mulungu, samafunsa kupereka zazing’ono pofuna kukwanitsa cifuniro ca Mulungu; samafunsa mbendela ya pafupi, koma amayang’anira ku muyeso wamphumphu wa cifuniro ca Mombolo wawo. Ndi cifuniro coona amapereka zonse, naonetsera cikondwerero colingana ndi mtengo wa cinthu cimene iwo ali kufuna. Kungobvomereza Kristu wopanda cikondi cakuyaci, ndi kungolankhula cabe, cipembedzo couma, ndi nchito yotopetsa.MOK 31.5

  Kodi uli kuti nsembe ya kupereka zonse kwa Kristu yakulitsa? Tadzifunsa wekha cifunso ici, “Kodi Kristu anapereka ciani cifukwa ca ine?” Mwana wa Mulungu anapereka zonse — moyo, cikondi, ndi masautso—kutiombola ife. Kodi monga ifetu, anthu osayenera kulandira cikondi cacikuru cotere, ndi kukaniza kupereka mitima yathu kwa Iye? Kanthawi kali konse ka moyo wathu tiri kulandira madalitso a cisomo cace, ndipo cifukwa ca ici sitingathe kuzindikira kokwana kukula kwace kwa zoopsa ndi cisoni ku zimene tapulumutsidwamo. Kodi tingamuyang’ane Iye amene anapyozedwa ndi zoipa zathu, ndiye tingokhalabe olola kudana ndi cikondi cace ndi nsembe yace? Pa kuyang’ana kudzicepetsa kosaleka kwa Ambuye wa ulemerero, kodi ife tidzang’ung’udza cifukwa tingathe kulowa m’moyo ndi kulimbana ndi kudzicepetsa tokha?MOK 33.1

  Cifunso ca mitima yambiri yonyada ndico, “Cifukwa ciani ndifunika kulapa ndi kudzicepetsa ndisanatsimikize kuti ndalandiridwa ndi Mulungu?” Ine ndikusonyeza kwa Kristu. Iye anali wosacimwa, ndipo koposa izi, anali Mfumu ya kumwamba; koma cifukwa ca munthu anayesedwa ucimo kupulumutsa mtundu wonse. “Ndipo anawerengedwa pamodzi ndi olakwa; koma ananyamula macimo a ambiri, napembedzera olakwa.” (Yesaya 53: 12. )MOK 34.1

  Kodi m’mene timapereka zonsemo, ndiye timapereka ciani? — Mtima wodetsedwa ndi zoipa kuti Yesu auyeretse, kuutsuka ndi mwazi wace, ndi kuupulumutsa ndi cikondi cace cosayerekezeka. Komabe anthu amaganiza kuti ncolimba kupereka zonse! Ndimacita manyazi pakumva anthu ali kuzilankhula, ndiponso ndiri kucita manyazi kuzilemba.MOK 34.2

  Mulungu safuna kuti ife tisiye cimene cingaticite ife ubwino wopambana ngati tingacisunge. M’zonse zimene Iye acita amayang’anira ubwino wa ana ace. Mulungu afuna kuti onse amene sanasankhe Kristu akadazindikira kuti Iye ali ndi zinthu zambiri zabwino za kuwapatsa iwo koposa zimene ali kudzifunira okha. Munthu ali kucita zosalungama ndi zopweteka zazikuru kwa moyo wace pamene ali kucita ndi kuganiza mosiyana ndi cifuniro ca Mulungu. Cimwemwe ceni ceni sicingapezeke m’njira yokanizidwa ndi Iye amene adziwa zomwe ziri zabwino kwa ife, ndi amene amakonza nzeru zabwino kwa olengedwa ace. Njira ya kuswa malamulo ndi njira ya cisoni ndi cionongeko.MOK 34.3

  Ndi kucimwa kuganiza kuti Mulungu amakondwera kuona ana ace ali kusautsidwa. Kumwamba konse kumakondwera ndi cimwemwe ca anthu. Atate wathu wa kumwamba samatseka njira za cimwemwe kwa wolengedwa wace ali yense. Malamulo a kumwamba amatiuza ife kuti tisiye zoipa zimene zimadzetsa masautso ndi matsoka, zimene zimatitsekera ife khomo la kumwamba ndi la cimwemwe. Mombolo wa dziko amalandira anthu monga momwe ali, ndi zosowa zawo zonse, zosalungama zawo ndi zofooka zawo; ndipo sadzangowatsuka mu zoipa zokha ndi kuwapatsa ciombolo mwa mwazi wace, koma adzakwanitsa zokhumba-mtima za onse amene abvomera kubvala gori lace, ndi kunyamula katundu wace. Colinga cace ndico kupatsa mtendere ndi mpumulo kwa onse akudza kwa Iye kudzafuna mkate wa moyo. Iye afuna kuti ife tidzicita nchito zimene zingatsogolere mapazi athu ku madalitso a kumwamba amene anthu osamvera sangawalandire. Cimwemwe coona ca moyo ndiko kukhala ndi Yesu m’mitima yathu, amene ali ciyembekezo ca ulemerero.MOK 34.4

  Ambiri ali kufunsa, “Kodi ndidzipereka ndekha bwanji kwa Mulungu?” Iwe ufuna kuzipereka kwa Iye, koma uli wofooka mu mphamvu zako, ndiwe kapolo wa kukaika, ndi wolamulidwa ndi makhalidwe a moyo wako wocimwa. Malimbiko ako ndi malonjezano ako ali ngati zingwe za mcenga. Sungathe kulamulira maganizo ako, zofuna zako, cikondi cako. Podziwa kuti umaswa malonjezano ako, nulephera kucita zowinda zako zimafooketsa cilimbiko ca mwa iwe wekha, ndi kukuganizitsa kuti Mulungu sangathe kukulandira; koma usagwe mphwai. Cimene ufunika kuzindikira ndiyo mphamvu yoonadi ya cifuniro. Imeneyi ndiyo mphamvu yolamulira m’makhalidwe a munthu, mphamvu ya kusankha. Ciri conse catsamira pa kucita bwino kwa cifuniro. Mphamvu ya kusankha, Mulungu anaipereka kwa anthu, kuti adzicita nayo. Iwe sungathe kusintha mtima wako, sungathe mwa iwe wekha kupereka cikondi cace kwa Mulungu; koma ungathe kusankha kumtumikira Iye. Ungathe kumpatsa Iye cifuniro cako; pompo adzagwira nchito mwa iwe kufuna ndi kucita komwe monga mwa cikondwerero cace. Potero makhalidwe ako onse adzakhala mu ulamuliro wa Mzimu wa Kristu; cikondi conse cidzakhala mwa Iye, maganizo ako adzakhala ogwirizana ndi Iye.MOK 35.1

  Kulakala kucita zabwino ndi kuyera mtima ndi kwabwino; koma ngati ungolekera pompo, sizidzapindula kanthu. Ambiri adzataika kwina ali kuyembekeza ndi kufuna kukhala Akristu. Safikira pa kupereka cifuniro cawo kwa Mulungu. Sali kusankhiratu tsopano kukhala Akristu.MOK 35.2

  Utacita naco bwino cifuniro cako, moyo wako ungathe kusinthika kweni kweni. Pa kupereka cifuniro cako kwa Kristu, uli kudzilumikiza wekha ndi mphamvu ya kuposa maukulu onse ndi maufumu. Udzalandira mphamvu zocokera kumwamba za kukulimbitsa, ndipo potero, pakudzipereka tsiku ndi tsiku kwa Mulungu, udzakhoza kukhala moyo watsopano, moyo wa cikhulupiriro.MOK 35.3

  Larger font
  Smaller font
  Copy
  Print
  Contents