Loading...
Larger font
Smaller font
Copy
Print
Contents
 • Results
 • Related
 • Featured
No results found for: "".
 • Weighted Relevancy
 • Content Sequence
 • Relevancy
 • Earliest First
 • Latest First
  Larger font
  Smaller font
  Copy
  Print
  Contents

  MUTU 9—NCHITO NDI MOYO

  Mulungu ali kasupe wa moyo ndi wa kuunika ndi wa cimwemwe ku maiko onse. Monga mitsitsi ya kuwala yocokera ku dzuwa, monga mitsinje ya madzi yocokera ku kasupe wa moyo, madalitso amayenda kuturuka kwa Iye kunka kwa zilengedwe zace zonse. Ndipo kuli konse kumene kuli moyo wa Mulungu m’mitima ya anthu, udzaturukira kwa ena m’cikondi ndi kudalitsa.MOK 57.1

  Cimwemwe ca Mpulumutsi cinali kutukula ndi kuombola anthu otaika. Cifukwa ca ici sanauyesera moyo wace ngati wamtengo wapatali kwa Iye yekha, koma anapirira mtanda, nanyoza manyazi. Cotero angelo ali kugwira nchito masiku onse kukondweretsa ena. Cimeneci ndico cimwemwe cawo. Nchito imene mitima ya anthu odzikonda okha angaiyesere yonyozeka, kutumikira iwo amene ali oipitsitsa, ndi onyozeka m’makhalidwe awo, imeneyi ndiyo nchito ya angelo osacimwa. Mzimu wa Kristu wa cikondi codzipereka yekha nsembe, ndiwo mzimu umene uli kumwamba, ndipo ndiwo mtima wa cimwemwe cace. Umenewu ndiwo mzimu umene ati adzalandire otsatira ace, ndi nchito yomwe ati adzacite.MOK 57.2

  Pamene cikondi ca Kristu cilowa mu mtima, monga zonunkhira zokoma, sicingathe kubisika. Mphamvu yace yopatulika idzamveka m’mitima ya anthu onse amene tikomana nawo. Mzimu wa Kristu ukakhala mu mtima uli ngati kasupe m’cipululu, amene amatsitsimutsa zinthu zonse, ndi onse amene ali pafupi kuonongeka amafunafuna kumwa madzi ace amoyo.MOK 57.3

  Cikondi ca Kristu cidzaonekera pa kufuna kugwira nchito monga anagwira Iyeyo, kudalitsa ndi kukweza mtundu wa anthu. Cidzatitsogolera kukonda, kukoma mtima, ndi kumvera cifundo olengedwa onse a cisamaliro ca Atate wathu wa kumwamba.MOK 57.4

  Moyo wa Mpulumutsi pa dziko lapansi sunali moyo wa mtendere, ndi wodzisamalira yekha, koma Iye anagwira nchito ndi khama, moona mtima, ndi wosatopa kupulumutsa anthu otaika. Kuyambira m’khola la ng’ombe kufikira pa Golgota, Iye anatsata njira ya kudzikana, ndipo sanafuna kumasulidwa ku nchito yobvuta, maulendo opweteka, ndi nkhawa zotopetsa. Iye anati. “Mwana wa munthu sanadza kutumikiridwa, koma kutumikira, ndi kupereka moyo wace dipo la anthu ambiri.” (Mateyu 20:28.) Cimeneci ndico cinali ciyang’aniro cacikuru ca moyo wace. Zinthu zina zonse zinali zaciwiri ndi zakungothangata. Cakudya cace ndi cakumwa cace kunali kucita cifuniro ca Mulungu ndi kutsiriza nchito yace. Kudzikonda kunalibe mbali m’nchito yace.MOK 57.5

  Cotero iwo amene alandira cisomo ca Kristu adzakhala ofulumira kupereka nsembe iri yonse, kuti ena amene Kristu anawafera agawane nawo mphatso ya kumwamba. Adzacita zonse monga angathe kukometsa dziko cifukwa ca kukhala iwo momwemo. Mzimu woterewu ndico citsimikizo ca kukula kwa moyo wotembenuka koona. Munthu akadza kwa Kristu, msanga mumadza cifuniro mu mtima mwace ca kudziwitsa ena bwenzi lopambana limene walipeza mwa Yesu; coonadi ca kupulumutsa ndi ca kuyeretsa sicingathe kutsekeka mu mtima mwace. Ngati tabvekedwa ndi cilungamo ca Kristu, ndi kudzazidwa ndi cimwemwe ca Mzimu wace wa kukhala m’kati mwathu, sitidzakhoza kukhala cete. Ngati talawa ndi kuona kuti Ambuye ali wabwino, tidzakhala nako kanthu kakufotokoza. Monga Filipo pamene anapeza Mpulumutsi, ife tidzaitana ena kudza kwa Iye. Tidzafunafuna kuwaonetsera zokopa za Kristu, ndi zinthu zosaoneka za dziko lirinkudza. Tidzakhala ndi cifuniro cacikuru ca kutsata njira imene Yesu anayenda. Tidzalakalaka kuti iwo otizungulira aone “Mwana wa Nkhosa wa Mulungu, amene acotsa cimo lace la dziko lapansi.”MOK 58.1

  Ndipo nchito ya kudalitsa ena idzatidalitsa ife tomwe. Cimeneci ndico cimene anali kufuna Mulungu pakutipatsa ife mbali ya kucita mu nzeru ya ciombolo. Iye anawapatsa anthu mwai wopambana cimwemwe coposa, cimene Mulungu apereka kwa iwonso, kugawira anzawo madalitsowo. Umenewu ndiwo ulemu wopambana cimwemwe coposa, cimene Mulungu apereka kwa anthu. Iwo amene agwira cotero nchito za cikondi amadza pafupifupi ndi Mlengi wawo.MOK 58.2

  Akadafuna, Mulungu akadapereka uthengawu, ndi nchito ya utumiki wa cikondi, kwa angelo a kumwamba. Akadacita nazo zinthu zina za kutsirizira nchito yace. Koma cifukwa ca cikondi cace cosatha, Iye anasankha kutiyesa ife ogwira nchito pamodzi ndi Iye ndi Kristu, ndi angelo, kuti tigawane nawo madalitso, cimwemwe, kukwezeka kwa uzimu, zimene zimaturuka mu utumiki uwu wopanda kudzikonda.MOK 58.3

  Timakhala oyanjana ndi Kristu pa kusautsidwa naye pamodzi. Nchito iri yonse ya kudzipereka nsembe cifukwa ca ubwino wa ena, imalimbitsa mzimu wa kukoma mtima mu mtima mwa wopatsayo, ndi kumlumikizitsa iye ndi Mombolo wa dziko, amene “anali wolemera, koma anasanduka wosauka cifukwa ca inu, kuti inu, ndi kusauka kwace, mukakhale olemera.” Moyo wathu udzakhala dalitso kwa ife, ngati ife tingakwanitse cifuniro ca Mulungu m’mitima yathu.MOK 58.4

  Ngati ungagwire nchito monga Kristu afunira kuti akuphunzira ace adzicita, ndi kumpindulira miyoyo, udzamva mu mtima kuti usowa nzeru za zinthu za kumwamba, ndi kumva njara ndi ludzu la cilungamo. Udzamdandaulira Mulungu, ndipo cikhulupiriro cako cidzalimba, ndipo moyo wako udzamwa pa citsime ca cipulumutso. Pokomana ndi mabvuto ndi mayeso, adzakuthamangitsira ku Bible ndi ku pemphero. Udzakula m’cisomo ndi cidziwitso ca Kristu, ndipo udzakulitsa macitidwe abwino.MOK 59.1

  Mzimu wa nchito yopanda umbombo ya kuthangata ena, umapatsa makhalidwe okhazikika ofanana ndi Kristu, ndipo umadza ndi mtendere ndi cimwemwe kwa iye wakuulandira. Zifuniro zimadzutsidwa. Mulibe malo a ulesi ndi kudzikonda. Iwo amene acita naco cisomo ca Kristu adzakula ndipo adzakhala ndi mphamvu kugwira nchito ya Mulungu. Iwo adzaona za uzimu mwangwiro, adzakhala ndi cikhulupiriro colimba, cokula, ndi mphamvu yocuruka m’pemphero. Mzimu wa Mulungu, pogwira nchito mu mtima, udzayeretsa moyo kuti uyanjane ndi Mulungu. Iwo amene adzipereka okha cotero ku nchito yosadzikonda okha cifukwa ca ubwino wa ena, ali kugwiradi nchito ya cipulumutso cawo.MOK 59.2

  Njira imodzi yokha ya kukulira m’cisomo ndiyo kugwira nchito imene Kristu anatipatsa ife osaganizira za ife tokha, — kucita, monga mwa nzeru zathu, kuthangata ndi kudalitsa amene asowa cithangato cathu. Mphamvu zimadza ndi kucitacita; cangu ndiwo makhalidwe eni eni a moyo. Iwo amene ayesa kukhala moyo wa Cikristu pakungolandira madalitso amene amadza kwa iwo mwa cisomo, osacita kanthu kwa Kristu, ali kuyesa kukhala ndi moyo pa kungodya osagwira nchito. Ndipo anthu amene acita cotero adzafa mwa uzimu.MOK 59.3

  Munthu amene angakane kucita nazo ziwalo zace, posacedwa zidzakhala zopanda mphamvu zosatha kucita kanthu. Cotero munthu amene sacita nazo mphamvu zimene Mulungu anampatsa, samangolephera kokha kukula mwa Kristu, koma amataya mphamvu yomwe adalandira kale.MOK 59.4

  Mpingo wa Kristu ndiwo umene Mulungu adausankha kugwira nchito ya cipulumutso ca anthu. Nchito yace ndiyo kunyamula uthenga kunka nawo ku dziko lonse. Ndipo nchitoyo iri pa Akristu onse. Ali yense, monga mwa talente lace, ndi nthawi yace, akwanitse nchito ya Mpulumutsi. Cikondi ca Kristu, coonetsedwa kwa ife, citiyesa ife amangawa kwa onse amene samdziwa. Mulungu watipatsa ife kuunika, si kwa ife tokha, komanso kuwaunikira iwo.MOK 59.5

  Otsata Kristu akadakhala a maso ku nchito, kumene kuli mmodzi lero, kukadakhala zikwi, kulalikira uthenga m’maiko a akunja. Ndipo onse amene sakadakhoza kugwira nchitoyi ndi manja awo, mwenzi ali kuithangata ndi ndalama zawo, ndi cifundo cawo, ndi mapemphero awo. Ndipo m’maiko a Cikristu mukadakhala nchito yoposa yofuna miyoyo.MOK 60.1

  Sikufunika kuti titonka ku maiko a akunja, kapena kusiya mabanja athu, ngati nchito yathu iri kumeneko, pofuna kugwira nchito ya Kristu. Tingathe kugwira nchito ya Kristu, m’mabanja mwathu, mu mpingo, pakati pa amene tizolowerana nawo, ndi iwo amene tigwira nawo nchito.MOK 60.2

  Mbali yaikuru ya moyo wa Mpulumutsi wathu, anali m’nchito yotopetsa m’nyumba yopala matabwa ku Nazarete. Angelo otumikira anali kusamalira Ambuye wa moyo pamene Iye anali kuyenda pamodzi ndi atsamunda, ndi anchito osadziwika ndi osalemekezeka. Iye anali kukwanitsabe nchito yace mokhulupirika pamene anali kugwira nchito yace yonyozekayo monga pamene anali kuciritsa odwala, kapena, poyenda pa nyanja ya Galileya. Cotero, m’nchito ndi m’malo onyozeka a moyo, tiyende ndi kugwira nchito pamodzi ndi Yesu.MOK 60.3

  Mtumwi ati, “Yense, m’mene anaitanidwamo, abale, akhale momwemo ndi Mulungu.” (1 Akor. 7: 24. ) Munthu wanchito agwire nchito yace m’njira imene ingalemekeze Mbuye wace cifukwa ca kukhulupirika kwace. Ngati ali wotsata Kristu woona, adzanyamula cipembedzo cace mu kanthu kali konse kamene acita, ndi kuonetsera mzimu wa Kristu kwa anthu. Wogwira nchito ndi zitsulo angathe kukhala kazembe wa cangu ndi wokhulupirika wa Iye amene anagwira nchito m’moyo wodzicepetsa pakati pa mapiri a Galileya. Ali yense amene achula dzina la Kristu adzigwira nchito kotero kuti ena pakuona nchito zace zabwino alemekeze Mlengi ndi Mombolo wawo.MOK 60.4

  Ambiri amadziletsa kupereka mphatso zawo ku nchito ya Kristu cifukwa anzawo ali ndi mphatso ndi mwayi koposa zawo. Ambiri amaganiza kuti koma iwo okha amene ali ndi matalente ambiri ndiwo ayenera kupereka nzeru zawo ku nchito ya Mulungu. Ambiri amaganiza kuti matalente adaperekedwa kwa anthu ena a mwayi, koma ena sanawaitane kugwira nawo nchito kapena kulandira mphotho. Koma m’fanizo muja sadanene coinco. Pamene mwini nyumba anaitana akapolo ace, anampatsa munthu ali yense nchito yace.MOK 60.5

  Ndi mzimu wokonda tidzagwira nchito zonyozeka, “monga ngati kwa Ambuye.” (Akolose 3: 2. ) Ngati cikondi ca Mulungu ciri mu mtima, cidzaonekera m’moyo. Pfungo labwino la Kristu lidzatizungulira ife, ndipo citsanzo cathu cidzautsa, ndi kudalitsa ena.MOK 61.1

  Usalindire nthawi ina yabwino, kapena kuyembekeza luso loposa limene uli nalo usanapite kukagwira nchito ya Mulungu. Usaganize za zimene dziko liti liganizire za iwe. Ngati moyo wako wa tsiku liri lonse ucitira umboni za ungwiro ndi kulimbika kwa cikhulupiriro cako, ndipo ena natsimikizidwa kuti iwe ufuna kuwacitira zabwino, nchito yako sidzapita pa cabe.MOK 61.2

  Wakuphunzira wa Yesu, ngakhale ali wonyozeka ndi wosauka koposa onse angathe kukhala dalitso kwa ena. Kapena iwo sangadziwe kuti iwo ali kucita kanthu kabwino, koma ndi cikoka cawo cosadziwika, iwo angayambitse mafunde a madalitso amene adzakulirakulira, ndi kubala zipatso zodala zimene iwo sangazidziwe, kufikira tsiku limene adzalandira mphotho yotsiriza. Iwo sali kumva kapena kudziwa kuti ali kucita cinthu cacikuru. Iwo samadzibvutitsa okha ndi kudera nkhawa za kupambana. Iwo amayenda kacetecete, namacita mokhulupirika nchito imene Mulungu awapatsa, ndipo moyo wawo sudzapita pacabe. Miyoyo yawo idzakulakulabe m’cifaniziro ca Kristu; iwo ali anchito anzace a Mulungu m’moyo uno, ndipo motero ali kukwanira kudzalandira nchito yaikuru ndi cimwemwe cosadetsedwa ca moyo ulinkudza.MOK 61.3

  Larger font
  Smaller font
  Copy
  Print
  Contents