Loading...
Larger font
Smaller font
Copy
Print
Contents
 • Results
 • Related
 • Featured
No results found for: "".
 • Weighted Relevancy
 • Content Sequence
 • Relevancy
 • Earliest First
 • Latest First
  Larger font
  Smaller font
  Copy
  Print
  Contents

  MUTU 2—WOCIMWA ASOWA KRISTU

  Munthu poyamba anapatsidwa mphamvu zambiri ndi malingaliro abwino. Anali wangwiro m’makhalidwe ace ndi wogwirizana ndi Mulungu. Maganizo ace anali angwiro, ziyang’aniro zace zinali zopatulika. Koma cifukwa ca kusamvera, mphamvu zace zinaipitsidwa, ndipo umbombo unalowa m’malo mwa cikondi. Makhalidwe ace anafooka kwambiri cifukwa ca ucimo, kotero kuti cinali cosatheka, mu mphamvu yace yokha, kukaniza mphamvu ya zoipa. Anayesedwa kapolo wa Satana, ndipo akadakhalabe comweco nthawi zonse Mulungu akadapanda kuletsa. Cifuniro ca Satana cinali ca kuononga nzeru ya Mulungu ya kulenga munthu, nadzaza dziko ndi tsoka ndi cipululu. Ndipo iye akadanena kuti zoipa zonsezi zacitika cifukwa ca nchito ya Mulungu pa kulenga munthu.MOK 13.1

  M’makhalidwe ace osacimwa, munthu anali kulankhula ndi Iye “amene zolemera zonse za nzeru ndi cidziwitso zibisika mwa Iye.” (Akolose 2: 3. ) Atacimwa, sanapezenso cikondwero m’kuyera, ndipo iye anafuna kubisala osafuna kuonana ndi Mulungu. Mtima uli wonse wosakonzedwa makhalidwe ace ndi wotere. Sulumikizana ndi Mulungu ndipo sukondwera kulankhula naye. Wocimwa sangakondwe pa maso pa Mulungu. Atakhala pakati pa angelo oyera athawapo. Monga ataloledwa kulowa kumwamba, sakapezako cimwemwe. Moyo wace sungabvomerezane ndi cikondi copanda umbombo cimene cimalamulira kumeneko, cifukwa mtima wa munthu ali yense umabvomerezana ndi mtima wa cikondi wa Mulungu. Maganizo ace, zokondweretsa zace, zidzakhala za cilendo kwa anthu opanda ucimo okhala kumeneko. Nyimbo yace singagwirizane ndi nyimbo ya kumwamba. Kwa iye kumwamba kudzakhala malo a mazunzo; adzidzafuna kubisala pa maso pa Iye amene ali kuwala kwace ndi cimwemwe cace. Si cifukwa ca kuti Mulungu saweruza molungama cimene cidzawaletse ocimwa kulowa kumwamba: adzatsekedwa kunja cifukwa ca kuti sali oyenera kulowako. Ulemerero wa Mulungu udzakhala moto wonyeka kwa iwo. Iwo adzakondwera kuonongedwa kuti abisale ku nkhope ya Iye amene anafa kuwaombola.MOK 13.2

  Kuli kosatheka kwa ife tokha kupulumuka m’dzenje la zoipa m’mene tamira. Mitima yathu iri yoipa ndipo ife sitingathe kuisintha. “Adzaturutsa coyera m’cinthu codetsa ndani? nnena mmodzi yense.” “Cifukwa cisamaliro ca thupi cidana ndi Mu- lungu; pakuti sicigonja ku cilamulo ca Mulungu, pakuti sicikhoza kutero.” (Yobu 14: 4; Aroma 8: 7. ) Sukulu, cifuniro ndi kuyesa kwa munthu, zonse ziri ndi nchito yawo koma zonsezo ziribe mphamvu. Kapena zingathe kukometsa kunja kokhaku, koma sizingathe kusintha mtima; sizingathe kuyeretsa kasupe wa moyo. Anthu asanasinthike ku ucimo kunka kukuyera, mphamvu idzigwira nchito m’kati mwawo ndipo mudzilowa moyo watsopano wocokera kumwamba. Mphamvuyo ndiye Kristu. Cisomo cace cokha ndico cingathe kupatsa moyo ku mitima ndi kuikokera kwa Mulungu ndi ku ungwiro. Mpulumutsi anati “Ngati munthu sabadwa kucokera kumwamba,” ngati salandira mtima watsopano, cifuniro catsopano, nchito zatsopano, ndi makhalidwe atsopano, otsogolera ku moyo watsopano, “iye sangathe kuona ufumu wa Mulungu.” ((Yohane 3: 3. ) Ganizo la kuti ndi cofunika kukulitsa ubwino umene uli mwa cibadwidwe ca munthu ndi cinyengo coipa. “Koma munthu wa cibadwidwe ca umunthu salandira za Mzimu wa Mulungu: pakuti aziyesa zopusa; ndipo sakhoza kuzizindikira, cifukwa ziyesedwa mwa uzimu.” “Usadabwe cifukwa ndinati kwa iwe, Uyenera kubadwa mwa tsopano.” (1 Akor. 2: 14; Yohane 3: 7. ) Za Kristu zinalembedwa, “Mwa Iye munali moyo ndipo moyo unali kuunika kwa anthu,” “ndipo palibe dzina lina pansi pa thambo la kumwamba lopatsidwa mwa anthu limene tiyenera kupulumutsidwa nalo.” (Yohane 1: 4; Mac. 4: 12. )MOK 13.3

  Siziri zokwana kungoona kukoma mtima kwa Mulungu, cikondi, cisamaliro ca Utate, ndi makhalidwe ace. Siziri zokwana kuzindikira nzeru ndi kulungama kwa malamulo ace, kuona kuti anakhazikika pa maziko osatha a cikondi. Paulo mtumwi anaona zonsezi pamene anati, “Ndibvomerezana naco cilamulo kuti ciri cabwino.” “Cotero cilamulo ciri coyera, ndi cilangizo cace ncoyera, ndi colungama ndi cabwino.” Koma ananenanso m’kusautsidwa ndi kuthedwa nzeru kwa moyo wace, “Koma ine ndiri wa thupi, wogulitsidwa kapolo wa ucimo.” (Aroma 7: 16, 12, 14. ) Iye analakalaka ungwiro, cilungamo, zimene analibe mphamvu mwa iye yekha kuzilandira, ndipo iye anapfuula, “Munthu wosauka ine! adzandilanditsa ndani m’thupi la imfa iyi?” (Aroma 7: 24. ) Kulira kotereku kunaturuka m’mitima yolemedwa m’maiko onse ndi m’mibadwo yonse. Kwa anthu onsewo kulipo kuyankha kumodzi kokha, “Taonani Mwana wa Nkhosa wa Mulungu amene acotsa cimo lace la dziko lapansi.” (Yohane 1: 29. )MOK 14.1

  Ambiri ali zithunzithunzi zimene Mzimu Woyera afuna ku- fotokozera coonadi ici, ndi kucifotokozera miyoyo imene ifuna kumasulidwa ku katundu wa zoipa. Pamene Yakobo anali kuthawa ku nyumba ya atate wace, atacimwa pa kunyenga Esau, iye analemedwa pa kuzindikira ucimo wace. Popeza anali yekha yekha, wolekanitsidwa ndi zonse za kukondweretsa moyo wace, ganizo lalikuru loposa onse mu mtima mwace, linali la kuopa kuti ucimo wace wamulekanitsa ndi Mulungu, ndi kuti wakanidwa ndi Mulungu. Mwa cisoni anagona pansi kupumula, pakati pa mapiri, ndi nyenyezi ziri kuwala kumwamba. Pamene anali mtulo, kuwala kozizwitsa kunadza m’masomphenya ace, ndipo taonani, pa dambo pamene iye adagona padaoneka ngati paima makwerero opita kumwamba ndipo angelo a Mulungu anali kukwera natsika pamenepo pamene kucokera mu ulemerero pamwamba, mau a Yehova anamveka ali kunena uthenga wa cisangalatso ndi ciyembekezo. Cimene cinakwanitsa cosowa ndi cilakolako ca moyo wa Yakobo cinaperekedwa cotero kwa iye, — Mpulumutsi. Ndi cimwemwe ndi kuthokoza anaona njira yotseguka imene iye, wocimwa, anapeza mwai wa kulankhula ndi Mulungu. Makwererowo anali kutanthauza Yesu amene ali Mnkhoswa woima pakati pa Mulungu ndi anthu.MOK 14.2

  Cimeneci ndi cithunzithunzi cimodzimodzi cimene Yesu anali kunena polankhula ndi Natanieli, pamene anati, “Mudzaona thambo lotseguka, ndi angelo a Mulungu atsika nakwera pa Mwana wa munthu.” Yohane 1: 51. ) Pa mpatuko uja, munthu anadzilekanitsa yekha ndi Mulungu; dziko lapansi linalekana ndi kumwamba. Cifukwa ca phompho limene linali pakati, panalibenso kulankhulana. Koma mwa Kristu, dziko lapansi lalumikizananso ndi kumwamba. Mwa ubwino wace, Kristu anasanja phompho limene linacitika ndi ucimo, kuti angelo otumikira adzilankhulana ndi munthu. Kristu alumikizanitsa munthu wakugwa, m’kufooka kwace ndi m’kulephera kwace ndi Kasupe wa mphamvu yosatha.MOK 15.1

  Anthu sangathe kupambana, ngakhale ayesetse kudzuka, anthu sangathe, ngati iwo akana kasupe wa ciyembekezo ndi cithangato kwa mtundu wakugwawu. “Mphatso iri yonse yabwino, ndi cininkho ciri conse cangwiro.” (Yakobo 1: 17) zicokera kwa Mulungu. Popanda Iye palibe munthu angathe kukhala ndi makhalidwe angwiro. Njira yopita nayo kwa Mulungu ndiyo Kristu yekha. Iye ati, “Ine ndine Njira, ndi Coonadi, ndi Moyo: palibe munthu adza kwa Atate koma mwa Ine.” (Yohane 14: 6. )MOK 15.2

  Mtima wa Mulungu ulirira ana ace a dziko lapansi ndi ciko- ndi colimba koposa imfa. Pa kupereka Mwana wace, anatikhuthulira ife kumwamba konse mu mphatso imodzi yomweyo. Moyo wa Mpulumutsi ndi imfa yace ndi kupembedzera kwace, utumiki wa angelo, kudandaulira kwa Mzimu, Atate wakugwira nchito pamwamba pa zonse ndi mwa zonse, cikondi cosaleka ca anthu a kumwamba, — onsewa amagwirizana kuthangata ciombolo ca munthu.MOK 15.3

  Anthuni! Tiyeni tiganize za nsembe yodabwitsa imene idaperekedwa cifukwa ca ife! Tiyeni tiyese kuyamika nchito ndi cangu cimene Mulungu ali kucita pa kubwezanso otaikawo ndi kuwabwezera ku nyumba ya Atate. Zokopa zolimba cotere, ndi mphamvu zotere, sizingapezeke zoposa izi; mphotho kwa amene acita zabwino, kukalowa kumwamba, kukhala pamodzi ndi angelo, ciyanjano ndi cikondi ca Mulungu ndi Mwana wace, kukwezeka ndi kukula kwa mphamvu zathu zonse kwa nthawi zonse, — kodi zimenezi sizolimbitsa mtima zokwana kutiumiriza ife kupereka nchito ya mtima wofuna kwa Mlengi wathu ndi Mpulumutsi?MOK 16.1

  Ndiponso maweruzo a Mulungu otsutsana ndi ucimo, cilango cimene cirikudza, kuipitsidwa kwa makhalidwe athu, ndi cilango cotsiriza, zidalembedwa m’mau a Mulungu kuticenjeza ife kupewa nchito za Satana.MOK 16.2

  Kodi sitiyenera kusamalira cifundo ca Mulungu? Nanga akadacitanji koposa izi? Tiyeni tidziyanjanitse ndi Iye amene anatikonda ife ndi cikondi cozizwitsa. Tiyeni ticite nazo zinthu zimene anatipatsa, kuti tisandulike m’cifaniziro cace ndi kubwezeredwa ku ciyanjano ca angelo otumikira, ndi kuyanjana ndi kulankhulana ndi Atate ndi Mwana wace.MOK 16.3

  Larger font
  Smaller font
  Copy
  Print
  Contents