Loading...
Larger font
Smaller font
Copy
Print
Contents
 • Results
 • Related
 • Featured
No results found for: "".
 • Weighted Relevancy
 • Content Sequence
 • Relevancy
 • Earliest First
 • Latest First
  Larger font
  Smaller font
  Copy
  Print
  Contents

  MUTU 11—UBWINO WA PEMPHERO

  Mulungu amalankhula ndi ife kupyolera mwa cilengedwe ndi Mau ace, mwa ukulu wace, ndi mwa mphamvu ya Mzimu Woyera. Koma ndi zosakwana zimenezi; tifunikanso kutsanulira mitima yathu kwa Iye. Pofuna kuti tikhale naco cangu ndi moyo wa uzimu, tiyenera kulumikizana kweni kweni ndi Atate wathu wa Kumwamba. Kapena mitima yathu ingatembenukire kwa Iye; kapena inde tingamaganizire za nchito zace, za cifundo zace, ndi za madalitso ace; koma kumeneku si kulankhula naye. Kulankhula ndi Mulungu koma tidzimuuza Iye zinthu za moyo wathu weni weni.MOK 69.1

  Pemphero ndiko kuuza Mulungu zonse za mu mtima monga bwenzi lathu. Maka maka sicifukwa ca kuti Mulungu adziwe za mu mtimazo, koma kuti ife tikhoze kumlandira Iye. Pemphero silimatsitsira Mulungu kwa ife, koma limatikweza ife kunka kwa Iye.MOK 69.2

  Pamene Yesu anali pa dziko lapansi, anaphunzitsa akuphunzira ace kupemphera. Iye anawalangiza kupereka zosowa zawo za tsiku liri lonse kwa Mulungu, ndi kutaya pa Iye nkhawa zawo zonse. Ndipo citsimikizo cimene anawapatsa iwo ca kuti mapemphero awo adzamveka, ndi citsimikizo kwa ifenso.MOK 69.3

  Yesu mwini, pamene anali kukhala pakati pa anthu, kawiri kawiri anali kupemphera. Mpulumutsi wathu anadzilumikiza ndi zosowa ndi zofooka zathu, popeza anasanduka wopemphera ndi wodandaulira, kufuna mphamvu zatsopano kwa Atate wace, kuti aturuke wolimba kukomana ndi nchito ndi mayeso. Iye ndiye citsanzo cathu m’zinthu zonse. Mwa zofooka zathu Iye ndiye mbale wathu, “woyesedwa m’zonse monga momwe ife;” koma monga wopanda ucimo, makhalidwe ace anali opanda ucimo; Iye anapirira mabvuto ndi mazunzo a moyo m’dziko la ucimo. Umunthu wace unaliyesera pemphero cinthu cofunika ndi cabwino. Iye anapeza cisangalatso ndi cimwemwe pa kulankhula ndi Atate wace. Ndipo ngati Mpulumutsi wa anthu, Mwana wa Mulungu, anadziwa kuti asowa pemphero, anthu ofooka, ocimwa, ayenera kudziwa kuti afunika pemphero loona losalekeza, koposa Iye.MOK 69.4

  Atate wathu wa kumwamba ali kulindira kutipatsa ife cidzalo ca madalitso ace. Ndi mwai wathu kuganizira kwambiri za kasupe wa cikondi cosatha. Ncozizwitsa ndithu kuti ife timape- mphera pang’ono cotere! Mulungu ali wofulumira ndi wolola kumva pemphero la ana ace onyozeka, koma ife sitifuna kumuuza Mulungu zofuna zathu. Kodi angelo a kumwamba angaganize ciani za anthu osauka, ogonjera mayeso, pamene mtima wa Mulungu wa cikondi cosatha, uli kuwadandaulira iwo, ndi wofulumira kuwapatsa iwo koposa zimene angapemphe, kapena kuziganiza, koma iwo namangopemphera pang’ono cotere, ndi kacikhulupiriro kakang’ono cotere? Angelo amakonda kugwada pamaso pa Mulungu; amakonda kukhala pafupi ndi Iye. Iwo amaciyesera cimwemwe cawo copambana kulankhula ndi Jye. Koma ana a dziko lapansi, amene asowa kwambiri cithangato cimene Mulungu angawapatse, amayang’anika okwanitsidwa kungoyenda okha opanda kuwala kwa Mzimu wace, osatsagana naye kuli konse amukako.MOK 69.5

  Mdima wa woipayo umaphimba iwo amene aleka kupemphera. Mayeso onong’ona a mdaniyo amawanyenga iwo kucimwa; ndipo zonsezi zimacitika cifukwa iwo samapemphera monga Mulungu anawauza iwo. Kodi cifukwa ciani ana a Mulungu adzikana kupemphera, kwina pemphero liri mfungulo m’dzanja la cikhulupiriro yotsegulira nkhokwe ya kumwamba, kumene kuli cuma cosatha ca Mulungu? Wopanda pemphero losaleka, ndi kuyang’anira mwa cangu, tiri moopsa mwa kuti tidzayamba kugwa mphwayi ndi kupatuka pa njira ya coonadi. Mdaniyo masiku onse ali kufuna kutseka njira ya ku mpando wacifundo, kuti ife ndi pemphero ndi cikhulupiriro tisalandire cisomo ndi mphamvu ya kukana mayeso.MOK 70.1

  Alipo makhalidwe ace amene ife tingayembekezere kuti Mulungu adzamva ndi kuyankha mapemphero athu. Coyamba ndico kuti timve mu mtima kuti tisowa cithangato cocokera kwa Iye. Iye analonjeza, “Ndidzathira madzi pa amene ali ndi ludzu, ndi mitsinje pa nthaka youma.” (Yesaya 44: 3. ) Iwo akumva njara ndi ludzu la cilungamo, amene afunafuna Mulungu, adziwitsitse kuti adzakhuta. Mtima utseguke kulandira mphamvu ya Mzimu, ukaleka kutero sudzalandira madalitso a Mulungu.MOK 70.2

  Umphawi wathu uli kutipembedzera ife kopambana kwa Mulungu. Koma tiyenera kufunafuna Ambuye tokha, kuti aticitire zinthu zimenezi. Iye ati, “Pemphani, ndipo cidzapatsidwa kwa inu.” Ndipo “Iye amene sanatimana Mwana wace wa Iye yekha, koma anampereka cifukwa ca ife tonse adzalekeranji kutipatsanso ife zinthu zonse kwaulere pamodzi ndi Iye?” (Mateyu 7: 7; Aroma 8: 32. )MOK 70.3

  Ngati tingasamale zopanda pace m’mitima yathu; ngati ti- ngaumirire coipa ciri conse codziwika, Ambuye sadzatimvera; koma pemphero la mtima wolapa ndi wodzicepetsa masiku onse lidzalandiridwa. Pamene takonza macimo onse amene tiwadziwa, tikhulupirire kuti mapemphero athu adzayankhidwa. Ubwino wa ife tokha sungathe kutilandiritsa ife cisomo ca Mulungu; kuyenera kwa Yesu ndiko kudzatipulumutse ife, mwazi wace ndiwo uti udzatitsuke ife; komabe iripo nchito imene ife tiyenera kucita pofuna kulandiridwa.MOK 70.4

  Cinthu cina cimene cimapambanitsa pemphero ndico cikhulupiriro. “Iye wakudza kwa Mulungu adzikhulupirira kuti alipo, ndi kuti ali wobwezera mphotho iwo akumfuna Iye.” ( Heb. 11: 6. ) Yesu anati kwa ophunzira ace, “Zinthu ziri zonse mukazifuna ndi kuzipempha, khulupirirani kuti mwazilandira ndipo mudzakhala nazo.” (Marko 11: 24. ) Kodi timamkhulupirira Iye?MOK 71.1

  Citsimikizo cakuti, Ndipo ali wokhulupirika wakulonjezayo, ciri cacikuru ndi copanda malire. Ngati sitidalandire zinthu zomwe tapempha pa nthawi yomwe tapemphayo, tidzingokhulupirirabe kuti Ambuye wamva, ndi kuti adzayankha mapemphero athu. Ife ndife ocimwa ndi osaona za patsogolo kotero kuti nthawi zina timapempha zinthu zimene sizidzakhala madalitso kwa ife, ndipo Atate wathu wa kumwamba cifukwa ca cikondi amayankha mapemphero athu pa kutipatsa za ubwino wathu wopambana, — zimene ngakhale eni acefe tikazikonda, ngati ndi masomphenya a kumwamba tikadaona zinthu monga momwe ziri. Pamene mapemphero athu ayang’anika ngati sali kuyankhidwa, tingoumirira lonjezano; cifukwa nthawi ya kuyankha idzafikadi ndithu, ndipo tidzalandira madalitso amene tiwasowa koposa. Koma kunena kuti masiku onse pemphero lidzayankhidwa monga m’mene tapemphera, ndi kulandira cinthu ceni ceni cimene tacipempha, ndiko kumuyesa Iye. Mulungu ali wa nzeru sangaphophonyei, ndipo ali wabwino sangathe kumana kanthu kabwino kwa amene ayenda molunjika. Usaope kumkhulupirira Iye, ngakhale suona kuti mapemphero ako ali kuyankhidwa msanga msanga. Khulupirira lonjezano lace loona, “Pemphani, ndipo cidzapatsidwa kwa inu.” (Mateyu 7: 7. )MOK 71.2

  Ngati tingamacite uphungu ndi zokaika zathu ndi mantha athu, kapena kuyesayesa kupeza kanthu kamene sitingathe kukaona bwino lomwe, tisanakhale ndi cikhulupiriro, mabvuto ndi nkhawa zidzangocuruka. Koma ngati tidza kwa Mulungu, tiri kumva mu mtima kuti sitingathe kudzithangata tokha monga momwe tiri, ndipo modzicepetsa, ndi cikhulupiriro tifotokoza zosowa zathu kwa Iye amene nzeru zace ziri zosatha, amene amaona zonse, ndi amene amalamulira zonse ndi cifuniro cace ndi mau ace, Iye adzamva kulira kwathu, ndipo adzalola kuunika kuwala m’mitima yathu. Ndi pemphero loona mtima ife timalumikizana ndi mtima wa Mulungu. Ngakhale tipande kudziwa nthawi imene Mombolo wathu ali kuwerama kuticitira cifundo ndi kutikonda ife, koma ziri zoonadi. Ngakhale tipande kumva kapena kuona kukhudza kwace, koma dzanja lace liri pa ife kutikonda ndi kutisamalira ife.MOK 71.3

  Pamene tidza kwa Mulungu kudzapempha cifundo ndi madalitso, tidzikhala nawo mzimu wa cikondi ndi wokhululukira m’mitima yathu. Tingathe bwanji kupemphera, “Mutikhululukire ife mangawa anthu, monga ifenso takhululukira a mangawa athu” (Mateyu 6: 12), kwina tiri nawo mzimu wosakhululukira? Ngati tiyembekeza kuti mapemphero athu amveke, tidzikhululukira anzathu cimodzimodzi monga ‘m’mene ife tiyembekeza kukhululukidwa.MOK 72.1

  Kucita khama m’pemphero ndiwo makhalidwe ena a kulandira. Ngati tifuna kukula m’cikhulupiriro ndi m’macitidwe tidzipemphera masiku onse. Ife “tidzilimbika cilimbikire m’kupemphera.” (“Citani khama m’kupemphera, nimudikire momwemo ndi ciyamiko.” (Aroma 12: 12; Akolose 4: 2. ) Petro awadandaulira okhulupirira, “Khalani anzeru, ndipo dikirani m’mapemphero.” (1 Petro 4: 7. ) Paulo atilangiza, “Komatu m’zonse ndi pemphero, ndi pembedzero pamodzi ndi ciyamiko, zopempha zanu zidziwike kwa Mulungu.” (Afilipi 4: 6. ) Yuda ati, “Koma inu, okondedwa, ndi kupemphera mu Mzimu Woyera, mudzisunge nokha m’cikondi ca Mulungu.” (Yuda 20, 21. ) Pemphero losaleka ndiyo mfundo yosaduka ya moyo ndi Mulungu, kotero kuti moyo wa Mulungu umadza m’moyo mwathu, ndipo m’moyo mwathu mumaturuka ungwiro ndi kuyera mtima kubwerera kwa Mulungu.MOK 72.2

  Kuli kufunika kucita cangu m’pemphero; kanthu kena kasakupingeni inu. Yesetsani kuti kulankhula kwanu kumveke pakati pa Yesu ndi moyo wanu. Funani nthawi iri yonse yabwino yakuti mupite kumene kuyenera kucitika pemphero. Iwo amene ali kufunafunadi kulankhula ndi Mulungu, adzaoneka m’misonkhano yopemphera, ali okhulupirika kugwira nchito yawo, ndi ofunitsitsa kupeza zokoma zonse angathe kuzipeza. Iwo adzapambanitsa nthawi iri yonse ya kudziika okha kumene angalandire kuwala kocokera kumwamba.MOK 72.3

  Tidzipemphera m’mabanja mwathu, ndipo koposa zonse, tisaleke pemphero la mtseri; cifukwa ndiwo moyo wa mzimu wathu. Nkosatheka kuti moyo ukule ngati tileka kupemphera. Pemphero la mu msonkhano ndi la m’banja liri losakwana. Mtseri, tiyeni titsegule mitima yathu pamaso pa Mulungu. Pemphero la mtseri limamvedwa ndi Mulungu yekha wakumva pemphero. Khutu la munthu silifunika kumva mapemphero otere. M’pemphero la mtseri moyo uli mu ufulu kopanda zosokosa ndi zokopa maso. Mwa cete, koma moona mtima pemphero limakafika kwa Mulungu. Zidzakhala zokoma ndi zokhalitsa, mphamvu zocokera kwa Iye amene aona mtseri, amene khutu lace liri lotseguka kumva pemphero locokera mu mtima. Ndi cikhulupiriro ca cete ndi kudzicepetsa, moyo umalankhula ndi Mulungu, ndi kusonkhanitsa kuwala kocokera kumwamba kuupatsa mphamvu ndi kuulimbitsa kumenyana ndi Satana. Mulungu ndiye nsanja yathu ya mphamvu.MOK 72.4

  Pemphera m’cipinda cako; ndipo pamene uli kugwira nchito yako, tukula mtima wako kwa Mulungu nthawi zonse. Enoke anayenda ndi Mulungu cotero. Mapemphero acetewa amakwera monga zonunkhira patsogolo pa mpando wa cisomo. Satana sangathe kumgonjetsa munthu amene mtima wace wakhazikika mwa Mulungu cotero.MOK 73.1

  Palibe nthawi kapena malo oti mtima wotere sungathe kupemphera kwa Mulungu. Palibe kanthu kangatiletse ife kutukula mitima yathu mu mzimu wa pemphero loona. M’makamu a anthu a mu mseu, pakati pa zinchito, tingatumize pemphero kwa Mulungu, ndi kumpempha kuti atitsogolere, monga anacita Nehemiya pamene anapereka pempho lace patsogolo pa Mfumu Aritasasta. Cipinda copempherera cingathe kupezeka kuli konse kumene tiri. Tidzitsegula khomo la mitima yathu kosaleka, ndi kumuitana Yesu kuti adze adzakhale monga mlendo wa kumwamba m’moyo mwathu.MOK 73.2

  Ngakhale potizungulira pali mpweya wowawa ndi wobvunda, sitifunika kupuma mpweya wace wowawawo, koma tingathe kupuma mpweya wangwiro wa kumwamba. Titsekere maganizo asaganize zonyansa ndi zoipa pa kutukula moyo wathu kunka pa maso pa Mulungu mwi pemphero loona. Iwo amene mitima yawo itseguka kulandira cithangato ndi dalitso la Mulungu adzayenda mu mpweya wopatulika koposa wa dziko lapansi, ndipo masiku onse adzalankhulana ndi Kumwamba.MOK 73.3

  Tisowa kumpenyetsetsa Yesu, ndi kuzindikira kokwana mtengo wa zinthu zosatha. Kukoma kwa kuyera mtima kuyenera kudzaze m’mitima ya ana a Mulungu; ndipo pofuna kucitika izi, tidzifunafuna cidziwitso ca zinthu za kumwamba.MOK 73.4

  Tiyeni tikweze moyo wathu kumwamba, kuti Mulungu atipatse ife mpweya wa kumwamba. Tiyeni tikhale pafupi ndi Mu- lungu, kuti mu yeso liri lonse lotidzidzimutsa maganizo athu atembenukire kwa Iye monga duwa limatembenukira ku dzuwa.MOK 73.5

  Onetsa zosowa zako, cimwemwe cako, zisoni zako, nkhawa zako, pamaso pa Mulungu. Sungathe kumlemetsa; sungathe kumtopetsa. Iye amene amawerenga tsitsi la pa mutu pako sali wosasamala zosowa za ana ace. “Ambuye ali wodzala cikondi ndi wacifundo.” (Yakobo 5: 11. ) Mtima wace wacikondi umakhudzidwa ndi zisoni zathu, ngakhale pamene tizinena. Muuze zonse zakubvuta mtima wako. Palibe cacikuru cosanyamulika ndi Iye, cifukwa Iye amagwiriziza maiko, amalamulira zonse m’maiko onse. Kali konse kotipatsa ife mtendere sikakhala kakang’ono pa maso pace. Palibe mau ena m’zolembedwa za macitidwe athu zimene ziri zozimirira kuti Iye sangathe kuziwerenga; palibe cobvuta cimene Iye sangathe kucikonza. Palibe cobvuta cimagwera ana ace, kapena nkhawa ya mtima, kapena cimwemwe, kapena pemphero, zimene Atate wathu saziona ndi kuzisamala msanga. “Aciritsa osweka mtima namanga mabala awo.” (Salmo 147: 3. ) Ciyanjano pakati pa Mulungu ndi moyo uli wonse ndi coona ndi codzaza monga ngati palibenso moyo wina umene Iye anaperekera Mwana wace wokondedwa.MOK 74.1

  Yesu anati, “Mudzapempha m’dzina langa; ndipo sindinena kwa inu kuti Ine ndidzakufunsirani inu kwa Atate; pakuti Atate yekha akonda inu.” “Ine ndinakusankhani inu... kuti cimene ciri conse mukapempha Atate m’dzina langa, akakupatseni inu.” (Yohane 16: 26, 27; 15: 16. ) Koma kupemphera m’dzina la Yesu kuli koposa kungochula dzinalo poyamba ndi pomariza pemphero. Koma kupemphera mu mtima ndi mu mzimu wa Yesu, tiri kukhulupirira malonjezano ace, kutsamira pa cisomo cace, ndi kugwira nchito zace.MOK 74.2

  Mulungu satanthauza kuti ali yense wa ife atokhala pa yekha ndi kudzipatula ku dziko m’malo mwa kudzipereka ku nchito za cipembedzo. Moyo udzikhala monga moyo wa Kristu, — pakati pa mapiri ndi makamu a anthu. Iye amene sacita kanthu kena koma kungopemphera, posacedwa adzaleka kupempherako, kapena mapemphero ace adzangosanduka ngati mwambo. Pamene anthu adzipatula m’moyo wa kusonkhana, ndi m’nchito ya Cikristu ndi kunyamula mtanda wace; pamene iwo aleka kugwira mokhulupirika nchito ya Mpulumutsi, amene anawagwirira nchito mokhulupirika, iwo amataya mutu wa pemphero, ndipo alibe mtima wa kudzipereka. Mapemphero awo amangokhala a iwo okha. Iwo sangathe kupempherera zosowa za anthu, kapena kumanga ufumu wa Kristu, kupempherera mphamvu zogwira nazo nchito.MOK 74.3

  Tiri kumwaza pamene ife sitigwirizana ndi kulimbitsana mphamvu ndi kulimbitsana mitima m’nchito ya Mulungu. Coonadi ca mau ace cimataya mphamvu yace ndi kufunika kwace m’mitima yathu. Mitima yathu imaleka kuwalitsidwa ndi kudzutsidwa ndi mphamvu yace ya kuyeretsa, ndipo timafa mwa uzimu. Timataya ciyanjano cathu ca Cikristu cifukwa ca kusowa kucitirana cifundo wina ndi mnzace. Iye amene ali kungodzitsekera kwa iye yekha sali kudzaza malo amene Mulungu afuna kuti iye adzaze. Ngati tingakuze ciyanjano cimene ciri m’makhalidwe athu cidzatiyanjanitsa ndi anzathu, ndipo cidzatikulitsa ndi kutilimbitsa ife m’nchito ya Mulungu.MOK 75.1

  Ngati Akristu angalumikizane pamodzi, namalankhulana za cikondi ca Mulungu, ndi za coonadi ca ciombolo, mitima yawo idzatsitsimuka, ndipo adzatsitsimutsana. Tidziphunzira zambiri tsiku liri lonse za Atate wathu wa kumwamba, ndi kupeza macitidwe atsopano a cisomo cace; pompo tidzafuna kulankhula za cikondi cace; ndipo pamene tiri kucita izi, mitima idzatenthedwa ndi kulimbitsidwa. Ngati tikadamaganiza ndi kulankhula zambiri za Yesu koposa za ife tokha, tikadakhala nawo maonekedwe ace ocuruka.MOK 75.2

  Tikadamaganiza za Mulungu kawiri kawiri, monga momwe timaona cisamaliro cace pa ife, mwenzi tiri kumsunga m’maganizo athu, ndi kukonda kulankhula za Iye, ndi kumlemekeza Iye. Timalankhula za dziko cifukwa timakondwera nazo. Timalankhula za abwenzi athu cifukwa timawakonda; zokondwa zathu ndi zisoni zathu zamangika pamodzi ndi iwo. Koma tiri ndi cifukwa cacikuru coyenera kukonda Mulungu koposa kukonda abwenzi athu a pa dziko lapansi; ndipo ciyenera kukhala cinthu cozolowereka koposa zonse m’dziko lapansi kumuyesa Iye woyamba m’maganizo athu onse, kulankhula za ubwino wace ndi kufotokoza za mphamvu zace. Mphatso zolemera zimene anatipatsa ife sizinali zakuti zimeze cikondi cathu ndi maganizo athu, kuti ife tisakhale ndi kanthu kakupereka kwa Mulungu; izo ziri za kutikumbutsa kosaleka za Iye, ndi kutimanga ife ndi nsinga za cikondi ndi kuyamika Atate wathu wa kumwamba. Tiri kuumiriritsa za dziko lapansi. Tiyeni titukule maso athu ku khomo lotseguka la kacisi wa kumwamba, kumene kuwala kwa ulemerero wa Mulungu kumawala m’nkhope ya Kristu, amene “akhoza kupulumutsa konse konse iwo akuyandikira kwa Mulungu mwa Iye.” (Heb. 7: 25. )MOK 75.3

  Tifunika kumlemekeza Mulungu kwambiri “cifukwa ca ubwino wace, ndi cifukwa ca nchito zace zodabwitsa kwa ana a anthu.” 2 (Salmo 107: 8. ) Macitidwe athu a cipembedzo asama- ngokhala kupempha ndi kulandira kokha. Tisamangoganizira za zosowa zathu zokha, osaganizanso za zabwino tiri kulandira. Si kuti tiri kupfempheretsai, koma kuti tiri kuperewera kupereka mayamiko. Tiri kulandira za cifundo za Mulungu masiku onse, koma timangomthokoza pang’ono pokha, timamtamanda pang’ono cifukwa ca zimene Iye waticitira ife.MOK 75.4

  Kale Yehova anauza Israyeli, pamene anasonkhana ku utumiki wace, “Muzidya pamaso pa Yehova Mulungu wanu, kukondwera nazo zonse mudazigwira ndi dzanja lanu, inu ndi a pa banja lanu, m’mene Yehova Mulungu wanu anakudalitsani.” (Deut. 12: 7. ) Cimene cicitika cifukwa ca kulemekeza Mulungu cidzicitika ndi cikondwerero, ndi nyimbo za kuyamika, osati ndi cis’oni.MOK 76.1

  Mulungu wathu ali Atate wacifundo. Utumiki wace usamayang’anidwa monga wobvuta ndi womvetsa cisoni. Cidzikhala cikondwero kupembedza Yehova, ndi kutenga mbali mu nchito yace. Mulungu safuna kuti ana ace, amene anawapatsa cipulumutso cacikuru cotere, kuti iwo adzicita ngati Iye ali Mbuye wobvuta wa nkharwe. Iye ndiye bwenzi lawo lopambana; ndipo pamene iwo ampembedza Iye, Iye ayembekeza kukhala nawo, kuwadalitsa ndi kuwasangalatsa iwo, ndi kudzaza mitima yawo ndi cimwemwe ndi cikondi. Yehova afuna kuti ana ace adzisangalatsidwa mu nchito yace, ndi kupeza cikondwerero koposa zobvuta mu nchito yace. Iye afuna kuti iwo amene adza kumpembedza Iye adzitenga maganizo abwino za cikondi cace ndi cisamaliro cace, kuti adzikondwera ndi nchito zorise za moyo wawo, kuti akhale ndi cisomo cakucita mokhulupirika ndi moona mtima m’zinthu zonse.MOK 76.2

  Tiyenera kusonkhana kuzungulira mtanda. Kristu ndi Iye wopacikwa adzikhala coganiza cathu cacikuru, colankhula cathu, ndi cimwemwe cathu copambana. Tidzisunga m’maganizo athu dalitso liri lonse limene talandira kwa Mulungu, ndipo pamene ife tizindikira cikondi cace cacikuru, tidzikhala olola kupereka kanthu kali konse ku dzanja limene linakhomeredwa pa mtanda cifukwa ca ife.MOK 76.3

  Moyo ukwere kuyandikira kumwamba ndi mapiko a ciyamiko. Mulungu amapembedzedwa ndi nyimbo m’mabwalo a kumwamba, ndipo pamene ife tiri kutsimikiza mayamiko athu, tiri kuyandikira ku cipembedzo ca angelo a kumwamba. “Wopereka nsembe ya ciyamiko andilemekeza Ine.” (Salmo 50: 23. ) Tiyeni, ndi cimwemwe colemekeza tidze patsogolo pa Mlengi wathu, ndi “mayamikiro ndi mau a nyimbo yok(? ma.” (Yesaya 51: 3. )MOK 76.4

  Larger font
  Smaller font
  Copy
  Print
  Contents