Loading...
Larger font
Smaller font
Copy
Print
Contents
 • Results
 • Related
 • Featured
No results found for: "".
 • Weighted Relevancy
 • Content Sequence
 • Relevancy
 • Earliest First
 • Latest First
  Larger font
  Smaller font
  Copy
  Print
  Contents

  MUTU 13—KUKONDWERERA MWA AMBUYE

  Ana a Mulungu aitanidwa kukhala oonetsera Kristu, kusonyeza ubwino ndi cifundo ca Ambuye. Monga Kristu anationetsera ife makhalidwe oona a Atate, cotero ifenso tinonetsere Kristu ku dziko losadziwa cikondi cace ndi cifundo cace. “Monga momwe munandituma Ine ku dziko lapansi,” anatero Yesu, “Inenso ndituma iwo ku dziko lapansi.” “Ine mwa iwo, ndi Inu mwa Ine,... kuti dziko lapansi lizindikire, kuti Inu munandituma Ine.” (Yohane 17: 18, 23. ) Mtumwi Paulo ati kwa akuphunzira a Yesu, “Popeza mwaonetsedwa kuti muli kalata wa Kristu,” “wodziwika ndi wowerengedwa ndi anthu onse.” (2 Akor. 3: 3, 2. ) Mwa mwana wace ali yense, Yesu amatumiza kalata ku dziko lapansi. Ngati uli wotsata Kristu, Iye watumiza kalata mwa iwe kunka ku banja, ku mseu, kumene iwe uli kukhala. Yesu, pokhala mwa iwe, afuna kulankhula ndi mitima ya iwo amene asanamdziwe. Kapena iwo sawerenga Bible, ndi kumva mau amene ali kulankhula nawo m’masamba ace; saona cikondi ca Mulungu mwa nchito zace. Koma ngati iwe uli woonetsera wa Yesu woona, kapena kupyolera mwa iwe iwo adzatsogozedwa kuzindikira za ubwino wace, nakopedwa kumkonda Iye ndi kumtumikira.MOK 83.1

  Akristu alikidwa monga onyamula miyuni pa njira ya kumwamba. Iwo adzionetsera ku dziko kuunika kumene kuli kuwala pa iwo kucokera kwa Kristu. Moyo wawo ndi makhalidwe awo adzikhala otero kuti kupyolera mwa iwo ena adziona mokoma za Kristu ndi nchito zace.MOK 83.2

  Ngati tionetseradi Kristu, tidzacititsa nchito yace kukhala yokopa monga momwe iri. Akristu amene amangocita cisoni m’moyo mwawo, namangong’ung’udza ndi kudandaula, ali kuwapatsa anzawo maonekedwe onyenga a Mulungu ndi a moyo wa Cikristu. Iwo ali kupereka citsimikizo ca kuti Mulungu sakondwera kuti ana ace adzikondwa, ndipo mwa ici amacitira umboni wonama kutsutsana ndi Atate wathu wa kumwamba.MOK 83.3

  Satana amakwezeka pamene iye angathe kutsogolera ana a Mulungu kusakhulupirira ndi kugwa mphwayi. Iye amakondwera kutiona ife tiri kuleka kukhulupirira Mulungu, tiri kukaika za kulola kwace ndi mphamvu zace za kutipulumutsa ife. Iye amakonda kuti ife tidziganiza kuti Yehova adzatipweteka ife ndi mphamvu zace. Nchito ya Satana ndiyo kuonetsera Ambuye ngati wopanda cifundo. Iye amakhotetsa coonadi cace. Amadzaza mitima yathu ndi maganizo onyenga a za Mulungu; ndipo m’malo mwa kuti tidziganizira coonadi za Atate wathu wa kumwamba, kawiri kawiri timamangirira maganizo athu pa zonyenga za Satana, ndi kunyoza Mulungu pa kusamkhulupirira ndi kumng’ung’udzira. Satana afuna kuti moyo wa cipembedzo udzikhala wa cisoni. Iye afuna kuti udzionekera wa nchito ndi wobvuta; ndipo pamene Mkristu aonetsera m’moyo wace maonekedwe otere a cipembedzo, nayenso, cifukwa ca kusakhulupirira kwace, ali kucitanso bodza la Satana.MOK 83.4

  Ambiri, poyenda pa njira ya moyo, amangoganiza za zocimwa zawo ndi zolephera zawo ndi zogwiritsidwa mwala zawo, ndipo mitima yawo imangodzazidwa ndi cisoni ndi kugwa mphwayi. Pamene ndinali ku Europe, mlongo wina amene anali kucita zotere, ndi amene anali m’mabvuto akuru, analemba kwa ine, kundipempha mau a kulimbitsa mtima. Usiku wace nditalandira kale kalatayo, ndinalota kuti ndinali m’munda, ndipo amene anali kuoneka ngati mwini wa mundawo, anali kunditsogolera ine m’njira zace. Ndinali kusonkhanitsa maluwa ndi kukondwera ndi kununkhira kwawo, pamene mlongo ameneyu, amene anali kuyenda pa mbali panga, anandiitana kuti ndione minga yosaoneka imene inapinga mtsogolo mwace. Iye anali kungolira ndi kucita cisoni. Iye sanali kuyenda m’njira, kutsatira mtsogoleri, koma anali kuyenda pakati pa minga. “Mai’ne,” iye analira, “Kodi si za cisoni kuti munda wabwinowu udzionongeka ndi minga?” Pompo mtsogoleriyo anati, “Isiye mingayo, cifukwa ingokupweteka. Sonkhanitsa maluwawo.”MOK 84.1

  Kodi sanalipo maanga ena owala m’macitidwe ako? Kodi unalibe nthawi zina zimene mtima wako unali kugunda ndi cimwemwe pa kuyankha Mzimu wa Mulungu? Pamene uyang’ana m’mbuyo mwa macitidwe a moyo wako, kodi sumapeza macitidwe ena okondweretsa? Kodi malonjezano a Mulungu, sali ngati maluwa onunkhira, okula pa mbali iri yonse ya njira yako? Kodi sungalole kuti kukoma kwawo ndi kununkhira kwawo kudzaze mtima wako ndi cimwemwe?MOK 84.2

  Minga idzangokupweteka ndi kukumvetsa cisoni; ndipo ngati ungosonkhanitsa zokhazi, ndi kuzionetsa kwa ena, kodi pamodzi ndi kucepetsa ubwino wa Mulungu kwa iwe wekha, suli kuwaletsa iwo akukuzungulira kuyenda m’njira ya moyo?MOK 84.3

  Siciri ca nzeru kusonkhanitsa maganizo onse osakondweretsa a moyo wa kale, — zoipa zace ndi zolephera zace, — kuzilankhula ndi kulira cifukwa ca izo kufikira tigwa nazo mphwayi. Moyo wa kugwa mphwayi uli wodzazidwa ndi mdima, uli kudzitsekera wokha kuwala kocokera kwa Mulungu, ndiponso uli kuponya mthunzi pa njira ya ena.MOK 84.4

  Thokozani Mulungu cifukwa ca zithunzithunzi zowala, zimene wationetsera ife. Tiyeni tikundike pamodzi zitsimikizo zodala za cikondi cace, kuti tidziziyang’ana nthawi zonse. Mwana wa Mulungu kusiya mpando wa cifumu wa Atate wace, kubveka umulungu wace ndi umunthu, kuti apulumutse munthu ku mphamvu ya Satana; kutigonjetsera ife, kuwatsegulira anthu kumwamba, kuululira anthu cipinda kumene Mulungu amaonetsera ulemerero wace; kutukulidwa kwa mtundu wolephera kuuturutsa m’dzenje limene ucimo udauponyamo, ndi kuyanjanitsidwanso ndi Mulungu wosatha, ndipo atapirira yeso la kumwamba mwa cikhulupiriro ca mwa Mombolo wathu, abvekedwa m’cilungamo ca Kristu, ndi kukwezedwa kunka ku mpando wace wa cifumu — izi ndizo zithunzithunzi zimene Mulungu afuna kuti tidziziganizira.MOK 85.1

  Pamene tiri kukaika za cikondi cace, ndi kusakhulupirira malonjezano ace, tiri kumnyoza Iye ndi kumvetsa cisoni Mzimu wace Woyera. Kodi mai nkumva bwanji za ana ace amene masiku onse ali kungodandaula za iye, monga ngati iye sali kuwacitira zabwino, kwina moyo wace wonse ali kuyesetsa kuwacitira zabwino ndi za kuwasangalatsa? Kapena atakaika za cikondi cace; mtima wace udzasweka. Kodi kholo liri lonse nkumva bwanji ngati ana ace alicitira cotero? Nanga Atate wathu wa kumwamba adzaganiza bwanji za ife, pamene ife sitikhulupirira cikondi cace, cimene cinamtsogolera Iye kupereka Mwana wace wobadwa yekha, kuti ife tipeze moyo? Mtumwi alerriba cotere, “Iye amene sanatimana Mwana wace wa yekha, koma anampereka cifukwa ca ife tonse, adzalekeranji kutipatsanso ife zinthu zonse pamodzi ndi iye?” (Aroma 8: 32. ) Ndipo cikhalirebe ambiri, ndi nchito zawo, ngakhale sali kunena ndi mau awo, ali kunena kuti, “Ambuye sali kutanthauza izi kwa ine. Kapena akonda ena, koma sandikonda ine.”MOK 85.2

  Zonsezi ziri kupweteka moyo wako womwe; cifukwa mau ali onse akukaika amene uli kulankhula, ali kuitana mayeso a Satana; ali kungokulimbikitsa kukaika, ndipo ali kukucotsera angelo otumikira. Pamene Satana akuyesa, usalankhule mau a kukaika kapena a mdima. Ngati usankha kumtsegulira, mtima wako udzadzazidwa ndi kusakhulupirira ndi mafunso opanduka. Ngati ulankhula maganizo ako, kukaika kuli konse kumene uli kulankhula si kumangobwerera pa iwe wekha, koma ndi mbeu imene idzamera ndi kubala zipatso m’moyo wa ena, ndipo cingadzakhale cosatheka kubweza citsanzo ca mau ako. Iwe wekha kapena ungapulumuke ku mayeso a Satana ndi ku msampha wace, koma ena, amene asocera ndi citsanzo cako, kapena sangakhoze kupulumuka ku kusakhulupirira kumene udawatsogolera. Nkofunika nanga kuti tidzilankhula zinthu zokhazokha za kupatsa mphamvu ndi moyo wa uzimu!MOK 85.3

  Angelo ali kumvetsera kuti amve mbiri imene uli kunyamula ku dziko za Ambuye wako wa kumwamba. Zolankhula zako zikhale za Iye amene ali nawo moyo wace cikhalire wa kukupembedzera kwa Atate. Ukagwira dzanja la bwenzi lako, m’milomo yako ndi mu mtima mwako mukhale zolemekeza Mulungu. Zimenezi zidzakopa maganizo ace kunka kwa Yesu.MOK 86.1

  Onse ali nawo mabvuto awo; za cisoni zobvuta kuzipirira, mayeso obvuta kuwakana. Usafotokoze mabvuto ako kwa anzako, koma fotokoza zonse kwa Mulungu m’pemphero. Uliyese lamulo lako kuti usalankhule konse ngakhale mau amodzi a kukaika kapena a kugwa mphwayi. Ungathe kucita zambiri kukondweretsa moyo wa ena ndi kulimbitsa nchito zawo, ndi mau a ciyembekezo ndi a cimwemwe coyera.MOK 86.2

  Alipo anthu ambiri olimba mtima amene ali kukanikizidwa ndi mayeso, ali pafupi kukomoka m’nkhondo yomenyana ndi cifuniro cawo ndi mphamvu ya zoipa. Usamgwetse mphwayi wotereyu m’nkhondo yace kobvuta. Mkondweretse ndi mau olimbika a ciyembekezo, akumlimbitsa pa njira yace. Potero kuwala kvva Kristu kudzawala mwa iwe. “Palibe wina wa ife akhala kvva iye yekha.” (Aroma 14: 7. ) Ndi citsanzo cathu cosadziwika ena adzalimbikitsidwa, kapena adzagwetsedwa mphwayi, ndi kulekana ndi Kristu ndi coonadi.MOK 86.3

  Alipo ambiri amene ali ndi maganizo oipa za moyo ndi makhalidwe a Kristu. Iwo amaganiza kuti Iye anali wopanda cikondi ndi cimwemwe, ndi kuti ali waukari, wa nkharwe, ndi wosakondwa. Mwambiri macitidwe onse a cipembedzo amacitidwa mawanga ndi maganizo acisoniwa.MOK 86.4

  Kawiri kawiri zimanenedwa kuti Yesu analira, koma sanaoneke ali kumwetulira. Zoonadi Mpulumutsi wathu anali munthu wa zisoni, ndi wozolowerana ndi zobvuta, cifukwa anatsegulira mtima wace ku matsoka a anthu. Koma ngakhale moyo wace unali wodzikana, ndi wakumva zowawa ndi nkhawa, mzimu wace sunaphwanyike. Nkhope yace sinali kuonetsa cisoni ndi kubvutika, koma inali ya mtendere. Mtima wace unali kasupe wa moyo; ndipo kuli konse kumene Iye anapita, ananyamula mtendere, cimwemwe ndi kukondwa.MOK 86.5

  Mpulumutsi wathu anali woona mtima ndi wolimbikira, koma sanali wa cisoni ndi wa nkhope yoti lende. Moyo wa iwo amene amtsanza Iye udzakhala wodzazidwa ndi nchito yoona mtima; iwo adzazindikira katundu wawo. Cimpepulo cidzacotsedwa; sikudzakhalapo kukondwa kodzitama, kapena kujeda kwa cipongwe; koma cipembedzo ca Yesu cimapatsa mtendere wonga mtsinje. Sicimacotsa kuwala kwa cimwemwe, sicimaletsa kukondwa, kapena kudetsa nkhope yosangalala. Kristu sanadze kutumikiridwa, koma kutumikira; ndipo pamene cikondi cace cilamulira mu mtima, tidzatsatira citsanzo cace.MOK 87.1

  Ngati ife tingamaganiziritse za kusakoma mtima ndi zosalungama za ena, tidzapeza kuti ncosatheka kuwakonda iwo monga Kristu anatikonda ife; koma ngati tingamaganiziritse za cikondi cozizwitsa ndi cifundo ca Kristu ca kwa ife, mzimu womwewo udzapitanso kwa ena. Tidzikondana ndi kucitirana ulemu, osasamala zifukwa ndi zophophonya zimene sitingalephere kuziona. Tidzikhala odzicepetsa ndi osadzikhulupira tokha, ndipo tidzikhala opirira ndi zoipa za ena. Zimenezi zidzapha umbombo wonse, ndi kutipanga ife a mtima wacifundo ndi wopatsa.MOK 87.2

  Davide ati, “Khulupirira Yehova, ndipo cita cokoma, khala m’dziko ndipo tsata coonadi.” (Salmo 37: 3. ) “Khulupirira Yehova.” Tsiku liri lonse liri nawo akatundu ace, nkhawa ndi zobvuta zace; ndipo pamene ife tikomana, timakhala ofulumira kulankhula za mabvuto athu ndi mayeso athu. Cotero mabvuto ambiri amene sali athu amalowa mu mtima, ndipo timacita mantha ambiri, ndi kulemedwa ndi nkhawa, kotero kuti wina nkuganiza kuti tiribe Mpulumutsi wacifundo, wokonda, wofulumira kumva zofunsa zathu, ndi kutikhalira ife thandizo lopezekeratu m’nthawi iri yonse ya kusowa.MOK 87.3

  Ena masiku onse ali kungoopa ndi kubwerekera mabvuto. Tsiku liri lonse amazingidwa ndi zizindikiro za cikondi ca Mulungu; tsiku liri lonse ali kulandira ubwino wace koma iwo sasamala madalitso amenewa. Mitima yawo nthawi zonse iri kungoganiza za kanthu kena koipa, kamene ali kuopa kuti kadzaoneka; kapena kobvuta kena kangaonekedi, kamene, ngakhale kali kakang’ono, kamatseka maso awo osaona zinthu zambiri zimene ayenera kuyamikira. Zobvuta zimene amakomana nazo, m’malo mwa kuti ziwapitikitsire kwa Mulungu, amene ali kasupe wa cithangato cawo, zimawalekanitsa ndi Iye, cifukwa iwo amangobvutika ndi kung’ung’udza.MOK 87.4

  Kodi tiri kucita bwino pa kukhala osakhulupirira cotero? Kodi cifukwa ciani tidzikhala osayamika ndi osakhulupirira? Yesu ndiye bwenzi lathu; Kumwamba konse kumakondwera kuticitira ife zabwino. Tisamalola zobvuta ndi nkhawa za tsiku liri lonse kubvuta mtima ndi kuticititsa tsinya. Ngati titero, masiku onse tidzakhala nako kanthu kakutibvuta ndi kutitopetsa. Tisamangocita nkhawa zimene zimangotibvuta ife ndi kutitopetsa, koma zosatithangata kupirira mayeso.MOK 87.5

  Ungakhale ubvutike m’nchito yako; ciyembekezo cako cimanka cideradera, nuopsedwa kuti udzataya; koma usagwe mphwayi taya nkhawa zako pa Mulungu, nungokhala cete ndi kukondwera. Pemphera nzeru kuti udzicita nchito yako mwa luso, ndipo potero, udzaletsa kutaika ndi kuonongekako. Cita zonse monga ungakhoze kupeza zabwino. Yesu analonjeza kuti adzatithangata, ngati ife tiyesetsa. Ngati, utatsamira pa Mthandizi wakoyo, wacita zonse monga ungathe, landira zomwe wapezazo mokondwa.MOK 88.1

  Si cifuniro ca Mulungu kuti anthu ace adziponderezedwa ndi nkhawa. Koma Ambuye wathu satinyenga ife. Samanena kwa ife, “Usaope; mulibe zoopsa m’njira mwako.” Iye adziwa kuti alipo mayesero ndi zoopsya, ndipo amacita nafe bwino lomwe. Iye samanena kuti adzawaturutsa anthu ace m’dziko la zoipali, koma amangowalozera ku cikopa cosalephera. Pemphero lace kwa akuphunzira ace linali la kuti, “Sindipempha kuti muwacotse iwo m’dziko lapansi, koma kuti muwasunge iwo kuletsa woipayo.” “M’dziko lapansi,” Iye anatero, “mudzakhala naco cibvuto; koma limbikani mtima; ndalilaka dziko lapansi Ine.” (Yohane 17: 15; 16: 33. )MOK 88.2

  M’ciphunzitso cace ca pa phiri, Kristu anaphunzitsa akuphunzira ace maphunziro a mtengo wapatari za kufunika kwace kwa kukhulupirira Mulungu. Maphunziro amenewa anaperekedwa kulimbitsa ana onse a Mulungu m’mibadwo yonse, ndipo afikira nthawi yathu ino odzazidwa ndi malangizo ndi cisangalatso. Mpulumutsi anawalozera akuphunzira ace mbalame za mlengalenga, pamene zinali kuyimba nyimbo zawo zoyamika, zosabvutika ndi nkhawa, cifukwa “sizimafesa ai, kapena sizimatema ai.” Ndipo cikhalirebe Atate wamkuru amazipatsa zosowa zawo. Mpulumutsi afunsa, “Nanga inu mulibe kusiyana nazo kuziposa kodi?” (Mateyu 6: 26. ) Wogawira Wamkuru wa munthu ndi nyama amatsegula dzanja lace, ndi kukhutitsa zilengedwe zace zonse. Amasamalira mbalame za mlengalenga. Samaponya cakudya m’milomo yawo, koma amazipatsa zosowa zawo. Zidzitola zokha zakudya zimene Iye adazimwazira. Zidzimanga zokha zisa zawo. Zidzidyetsa ana awo. Zimanka ziri kuyimba ku nchito yawo, cifukwa, “Atate wanu wa kumwamba azidyetsa.” Ndipo “Nanga inu mulibe kusiyana nazo, kuziposa kodi?” Kodi inu, anthu a nzeru, ompembedza mu mzimu, simuli a mtengo wapatari koposa mbalame za mlengalenga? Kodi Mlengi wathu, Wosungira wa moyo wathu, Yemwe anatilenga ife m’cifaniziro cace, sadzatipatsa ife zosowa zathu ngati ife timkhulupirira?MOK 88.3

  Kristu analozera akuphunzira ace maluwa a m’thengo okula bwino ndi onunkhira, ndi okongola mu ubwino umene Atate wa kumwamba anawapatsa monga citsimikizo ca cikondi cace kwa munthu. Iye anati, “Tapenyetsani maluwa a kuthengo makulidwe awo.” Kukongola kwa maluwa a kuthengowa kwapitirira ulemerero wa Solomo. Zobvala zokongola koposa, zopangidwa ndi anthu a luso, sizingathe kulingana ndi kukongola kwa maluwa amene Mulungu adawalenga. Yesu afunsa, “Koma ngati Mulungu abveka cotero maudzu a kuthengo, akhala lero, ndi mawa aponyedwa pa moto, nanga si inu kopambana ndithu, inu akukhulupirira pang’ono? (Mateyu 6: 28, 30. ) Ngati Mulungu, m’misiri wa kumwamba, amapatsa maluwa amene angoonongeka m’tsiku limodzi, maanga awo abwino osiyanasiyana, kodi sadzawasamalira kopambana iwo amene adawalenga m’cifanizo cace comwe? Phunziro la Yesuli liri kudzudzula mtima woda nkha-wa, wobvutika ndi wokaika, ndi wopanda cikhulupiriro.MOK 89.1

  Yehova afuna kuti ana ace onse amuna ndi akazi adzikhala okondwa, a mtendere, ndi omvera. Yesu ati, “Mtendere wanga ndikupatsani; Ine sindikupatsani inu monga dziko lapansi lipatsa. Mtima wanu usabvutike, kapena usacite mantha.” ‘‘Izi ndalankhula ndi inu, kuti cimwemwe canga cikhale mwa inu, ndi kuti cimwemwe canu cidzale.” (Yohane 14: 27; 15: 11. )MOK 89.2

  Cimwemwe cimene cimacokera mu umbombo, osati mu nchito, ncacabe ndi cosakhalitsa; cimangocoka, ndi kusiya moyo woungulumwa ndi wa cisoni; koma muli cimwemwe ndi kukwanitsidwa m’nchito ya Mulungu; Mkristu sadasiyidwe kuyenda m’njira zosadziwika; sadasiyidwe m’zisoni zopanda pace, ndi zogwiritsa mwala. Ngati sitilandira zokondweretsa za moyo uno, tidzingokondwerabe pa kuyembekezera moyo ulinkudza.MOK 89.3

  Koma ngakhale pansi pano Akristu adzakhala ndi cimwemwe ca kulankhula ndi Kristu; adzakhala ndi kuunika kwa cikondi cace, cisangalatso cosatha ca nkhope yace. Phazi liri lonse m’moyo lidzatitengera cifupi ndi Yesu, lidzatipatsa ife macitidwe oona a cikondi cace, ndipo tidzasuntha phazi limodzi kuyandikira kwathu kodala kwa mtendere. Tiyeni tsono, tisataye cilimbiko cathu, koma citsimikizo cathu cikhale colimba koposa kale. “Kufikira pano Yehova anatithandiza” (1 Sam. 7: 12), ndipo adzatithandizabe kufikira cimariziro. Tiyeni tiyang’ane ku zinthu zokumbutsa, zokumbutsa zimene Yehova anacita kutisangalatsa ndi kutipulumutsa ife ku dzanja la woonongayo. Tiyeni tikumbukire m’mitima yathu za cifundo zimene Yehova waticitira ife, — misozi imene waipukuta, zowawa zimene wazitonthoza, nkhawa zimene wazicotsa, mantha amene wacotsa, zosowa zimene watipatsa, madalitso amene wapereka, — potero tidzadzilimbitsa tokha kwa zonse zimene ziri patsogolo pathu kupyola kotsala kwa ulendo wathu.MOK 89.4

  Sitingathe kuleka kuyang’ana zobvuta zatsopano zimene ziri kudza m’nkhondo yathu ya mtsogolo, koma tiyenera kuyang’ana zam’mbuyo, cimodzimodzi za mtsogolo ndi kunena, “Kufikira pano Yehova anatithandiza.” “Monga masiku ako momwemo mphamvu yako.” (Deut. 33: 25. ) Mayeso sadzakhala optirira mphamvu zimene zidzapatsidwa kwa ife za kupirira nazo. Pompo tiyeni titenge nchito yathu komwe taipezera, tiri kukhulupirira kuti ciri conse comwe cingadze, adzatipatsa mphamvu zokwanira ndi mayesowo.MOK 90.1

  Ndipo patsogolo pace zipata za kumwamba zidzatsegulidwa kulowetsa ana a Mulungu, ndipo m’milomo ya Mfumu ya ulemerero mudzaturuka dalitso longa nyimbo yokometsetsa, “Idzani kuno inu odalitsika a Atate wanga, lowani mu ufumu wokonzedwera kwa inu pa cikhazikiro cace ca dziko lapansi.” (Mateyu 25: 34. )MOK 90.2

  Pompo oomboledwa adzaloledwa kulowa m’zinyumba zimene Yesu ali kuwakonzera. Kumeneko anzawo sakakhala zonyenga za dziko, a mabodza, opembedza mafano, onyansa, ndi osakhulupirira; koma akazolowerana ndi iwo amene anagonjetsa Satana, ndi amene mwa cisomo ca Mulungu anapanga makhalidwe angwiro. Coipa ciri conse, conyansa ciri conse cimene cinali kuwabvuta pansi pano, cinacotsedwa ndi mwazi wa Kristu, ndipo ukulu ndi kuwala kwa ulemerero wace, wowala koposa dzuwa, udzapatsidwa kwa iwo. Ndipo makhalidwe ace abwino ndi angwiro adzawala mwa iwo koposa kunja kwawo. Adzakhala opanda cifukwa patsogolo pa mpando wacifumu woyera, ali kugawana nawo ulemu ndi mwayi wa angelo.MOK 90.3

  Poyang’ ana cuma ca ulemerero cimene cidzakhala cace, “Kodi munthu adzaperekanji cosintha naco moyo wace?” Mateyu 16: 26. ) Ngakhale ali wosauka, koma adzalandira mwa iye yekha cuma ndi ulemu zimene dziko silingathe kumpatsa. Moyo woomboledwa ndi wotsukidwa mu zoipa, ndi mphamvu zace zonse zoperekedwa ku utumiki wa Mulungu, uli wa mtengo wapatari; ndipo kuli cimwemwe m’mwamba pamaso pa Mulungu ndi angelo oyera cifukwa ca moyo umodzi woomboledwa, cimwemwe cimene cimatsimikizidwa m’nyimbo za cigonjetso coyera.MOK 90.4

  Larger font
  Smaller font
  Copy
  Print
  Contents