Loading...
Larger font
Smaller font
Copy
Print
Contents
 • Results
 • Related
 • Featured
No results found for: "".
 • Weighted Relevancy
 • Content Sequence
 • Relevancy
 • Earliest First
 • Latest First
  Larger font
  Smaller font
  Copy
  Print
  Contents

  MUTU 12—COCITA NAKO KUKAIKA

  AMBIRI, makamaka iwo amene ali atsopano m’moyo wa Cikristu, nthawi zina amabvutika ndi maganizo a cikaiko. Ziripo zinthu zambiri m’Bible zimene sangathe kuzifotokoza, kapena kuzimvetsetsa, ndipo Satana amacita ndi zimenezi kugwedeza cikhulupiriro cawo M’malembo monga ngati ndi bvumbulutso kocokera kwa Mulungu. Iwo amafunsa, “Kodi ndidzaidziwa bwanji njira yabwino? Ngati Bible ali Mau a Mulungudi, nanga ndidzamasulidwa bwanji ku zokaikazi ndi zobvutazi?MOK 77.1

  Mulungu samatiuza ife kukhulupirira, wosatipatsa umboni wokwana kukhazikapo cikhulupiriro cathu. Kukhazikika kwace, makhalidwe ace, coonadi ca mau ace, wonsewu ndi umboni wokhazikika umene umatitsimikizira m’mitima yathu; ndipo umboni umenewu uli wocuruka. Komabe Mulungu sanacotse zokaikitsa. Cikhulupiriro cidzikhazikika pa umboni osati pa zosonyeza. Iwo amene afuna kukaika adzaipeza nthawi; pamene iwo amene afunadi kudziwa coonadi, adzapeza umboni wokwana pokhazikitsapo cikhulupiriro cawo.MOK 77.2

  Ncosatheka nzeru za anthu kuzindikira kokwana makhalidwe kapena nchito za Mulungu Wosatha. Ngakhale kwa anzeru, ndi ophunziritsa, Woyerayo amaoneka mwa cimbuuzi ndi mwa cinsinsi. “Kodi ukhoza kupeza Mulungu mwa kufunafuna? Ukhoza kupeza Wamphamvuyonse motsindika? Kumpeza kutanimpha ngati kumwamba, ungacitenji? Kuzama ngati ku manda ungadziwenji?” (Yobu 11: 7, 8. )MOK 77.3

  Mtumwi Paulo ati, “Ha! kuya kwace kwa kulemera ndi kwa nzeru ndi kwa kudziwa kwace kwa Mulungu! Osasanthulikadi maweruzo ace, ndi njira zace nzosalondoleka!” (Aroma 11: 33. ) Koma ngakhale “pomzinga pali mitambo ndi mdima, cilungamo ndi ciweruzo ndizo zolimbitsa mpando wacifumu wace.” (Salmo 97: 2. ) Tingathe kuzindikira macitidwe ace ndi ife, ndi njira zimene agwira nazo nchito, kuti ife tizindikire cikondi ndi cifundo cosatha columikizana ndi mphamvu yosatha. Tingathe kuzindikira zambiri za nchito zace zonga zomwe ziri za ubwino wathu kuzidziwa; koma koposa izi tidzingozisiya m’manja okhoza kucita zonse, ndi mtima wodzala ndi cikondi.MOK 77.4

  Mau a Mulungu, monga makhalidwe a Mwini wace, amaonetsa zinsinzi zimene sizingathe kuzindikirika kokwana ndi anthu. Malowedwe a ucimo m’dziko, kubadwa m’thupi kwa Kristu, ku- badwanso, kuuka kvva akufa, ndi maphunzitso ena ambiri a m’Bible, ali zinsinsi zakuya zoti munthu sangathe kuzifotokoza, kapena kuzizindikira kokwana. Koma tiribe cifukwa ca kukaikira Mau a Mulungu cifukwa ca kuti sitingathe kuzindikira zinsinsi za ukuru wace. M’dziko lathu lomwe lino tazungulidwa ndi zinsinsi zimene sitingathe kuziyeza. Makhalidwe a moyo ngakhale ang’ono kwambiri ali obvuta kwambiri kotero kuti ngakhale anzeru kopambana alibe mphamvu kuwafotokoza. Kuli konse kuli zozizwa zimene sitingathe kuzidziwa. Nanga tidzizizwa kodi popeza kuti m’dziko la uzimu zirimonso zinsinsi zimene ife sitingathe kuziyeza? Bvuto lace makamaka liri m’kufooka ndi kucepa kwa nzeru za anthu. Mulungu anatipatsa ife M’malembo umboni wokwana za makhalidwe ace a umulungu, ndipo ife tisamakaika Mau ace cifukwa ca kuti sitingathe kuzindikira zinsinsi zonse za ukuru wace.MOK 77.5

  Mtumwi Petro ati kuti M’malembo “muli zina zobvuta kuzizindikira, zimene anthu osaphunzira ndi osakhazikika apotoza ... ndi kudziononga nawo eni.” (2 Petro 3: 16. ) Zobvuta za Malembo zimakakamizidwa ndi kukaika monga zokangana ndi Bible; koma sizotero konse, izo ndizo umboni wolimba kuti adaperekedwa ndi Mulungu. Mukadakhala mopanda ciwerengero ca Mulungu koma zimene tingathe kuzizindikira mofewa; ngati ukuru wace ndi ufumu wace ukadazindikirika ndi nzeru za anthu, Bible sakadanyamula umboni wosalakwa vva ulamuliro wa Mulungu. Kukoma kwace ndi cinsinsi cace ca mitu yolembedwamo, ziyenera kukulitsa cikhulupiriro cathu kuti ndiwo Mau a Mulungu.MOK 78.1

  Bible amaulula coonadi mofewa ndi mwangwiro moyenera zosowa ndi zolakalaka za mtima wa munthu, cimene cinadabwitsa anthu ophunzira kwambiri, kvvina cimathangata odzicepetsa ndi osaphunzira kuzindikira njira ya cipulumutso. Ndipo cikhalirebe coonadi cofewaci ciri ndi maphunzitso okwezeka, ofika patari osatha, opitirira nzeru za anthu, kotero kuti ife tingathe kuwalandira ivvo cifukwa Mulungu ndiye anawafotokoza. Ndimo m’mene nzeru ya ciombolo inatsegulidwira kwa ife kuti munthu ali yense aone mapazi amene ayenera kuponda pa kulapa kunka kwa Mulungu, ndi cikhulupiriro ca kwa Ambuye wathu Yesu Kristu, kuti tipulumustidwe mu njira yoikika ndi Mulungu; komabe pansi pa zoona izi; zozindikirika mofewa cotere, pali zinsinsi zimene zimabisa ulemerero wace, —zinsinsi zotopesta malingaliro pakuzifunafuna, koma zakumpatsa cikhulupiriro wakufunafuna coonadi ndi mtima woona. Akamasa- nthula Bible kvvambiri, atsimikizidwanso kwambiri kuti ndiwo mau a Mulungu wa moyo, ndipo ciweruzo ca munthu cimagonja patsogolo pa ukuru wa bvumbulutso la Mulungu.MOK 78.2

  Kuzindikira kuti sitingathe kuzindikira kokwana zoonadi zazikuru za Bible, uku ndiko kubvomera kuti nzeru za munthu wopita msanga siziri zokwana kuzindikira zosatha; kuti munthu, ndi nzeru zace zakutha msanga, za umunthu, sangathe kuzindikira nchito za Mulungu Wodziwa zonse.MOK 79.1

  Popeza sangathe kudziwa zinsinsi zace zonse, okaika ndi osakhulupirira amakana mau a Mulungu; ndipo si onse amene akhulupirira Bible ali opulumuka ku coopsa ici. Mtumwi ati, “Tapenyani, abale, kuti kapena ukakhale mwa wina vva inu mtima wcipa wosakhulupirira, wa kulekana ndi Mulungu wa moyo.” (Heb. 3: 12. ) Nkwabwino kuphunzira kolimba maphunzitso a Bible, ndi kusanthula “zakuya za Mulungu” (1 Akor. 2: 10), monga momvve ziri kuonetsedwa M’malembo. Ngakhale “zinsinsi nza Yehova Mulungu vvathu,” “zobvumbuluka nza ife.” (Deut. 29:29.) Koma ndi nchito ya Satana kupatutsa mphamvu ya kusankha ya mtima. Kunyada kumasanganizika ndi maganizo a coonadi ca Bible, kotero kuti anthu amakvviya ndi kugonjetsedwa ngati sangathe kufotokoza mbali iri yonse ya Malembo monga afuna. Ciri ca manyazi kwa iwo kubvomera kuti sali kumvetsetsa mau a Mulungu. Sali olola kulindira mopirira kufikira Mulungu adzaone kuti nkoyenera kuululira coonadi kwa iwo. Ivvo amaganiza kuti nzeru zawo zosathangatidwa za umunthu ziri zokwana kuwazindikiritsa iwo malembo, ndipo polephera kucita izi, iwo amakana konse ulamuliro wace. Nzoonadi kuti maganizo ndi maphunzitso amene anthu ambiri amaganiza kuti amacokera m’Bible alibe maziko awo m’maphunzitso ace, ndipo ndithu ali osiyana ndi mau a uzimu. Zinthu izi zidacititsa kukaika ndi nkhawa m’mitima yambiri. Koma sizimacitika cifukwa ca Mau a Mulungu, koma cifukwa ca kuti munthuyo ali kupotoza.MOK 79.2

  Cikadakhala cotheka kuti anthu olengedwa adzilandira nzeru zokwana kudziwa Mulungu ndi nchito zace, pompo atafika pamenepa, si bwenzi ali kupezanso coonadi, kapena kukula m’cidziwitso, kapena kukula m’malingaliro ndi mu mtima. Mulungu sakadakhalanso wamkulu; ndipo munthu, atafika cimaliziro ca cidziwitso, akadaleka kukula. Tiyeni tiyamike Mulungu kuti siziri zotero. Mulungu ali wosatha; mvva Iye muli “zolemera zonse za nzeru ndi cidziwitso.” (Akolose 2: 3. ) Ndipo ku nthawi zonse anthu ati adzidzangosanthula, namangophunzira, koma osatsiriza zolemera za nzeru zace, za ubvvino wace, ndi za mphamvu zace.MOK 79.3

  Mulungu afuna kuti ngakhale m’moyo uno coonadi ca Mau ace cidziululidwa kwa anthu ace. Iripo njira imodzi yokha imene tingalandirire cidziwitsoci. Tingathe kulandira cizindikiritso ca mau a Mulungu ndi kuunika kwa Mzimu amene anapereka Mauwo. “Zinthu za Mulungu palibe wina azidziwa, koma Mzimu wa Mulungu;” “pakuti Mzimu asanthula zonse zakuya za Mulungu zomwe.” (1 Akorinto 2: 10, 11. ) Ndipo lonjezano la Mpulumutsi kwa ophunzira ace linali, “Pamene atadza Iyeyo, Mzimu wa coonadi adzatsogolera inu mwa coonadi conse.... Pakuti adzatenga za kwa Ine nadzazilalikira kwa inu.” (Yohane 16: 13, 14. )MOK 80.1

  Mulungu afuna kuti munthu adzicita nazo mphamvu zace za kuganiza; ndipo kuphunzira Bible kudzalimbitsa ndi kudzutsa malingaliro koposa kuphunzira kanthu kena. Ngati sitifuna kuti Malembo angokundikana m’malingaliro athu, kotero kuti sitingathe kuzindikira coonadi cace, tidzikhala ndi cikhulupiriro conga ca mwana, ofulumira kuphunzira, ndi kupempha cithangato ca Mzimu Woyera. Pozindikira mphamvu ndi nzeru za Mulungu, ndi kuperewera kwathu kuzindikira ukuru wace, zidzitidzaza ife ndi kufatsa, ndipo tidzitsegula mau ace, monga tiri kulowa pamaso pace, ndi kuopa koyera. Pamene tidza ku Bible, maganizo adzizindikira ulamuliro waukuru koposa, ndipo mtima ndi nzeru zidzigwadira INE NDINE wamkuru.MOK 80.2

  Ziripo zinthu zambiri zobvuta kapena zobisika, zimene Mulungu adzazifotokoza ndi kuzifewetsa kwa iwo amene afuna kuzizindikira. Koma wopanda citsogozo ca Mzimu Woyera, tidzingopotozabe Malembo. Ziripo zowerenga zambiri za Bible zimene sizipindulitsa, ndipo mwambiri zimapweteka kopambana. Pamene Mau a Mulungu atsegulidwa wopanda ulemu ndi wopanda pemphero; pamene maganizo ndi cikondi sizimangirira pa Mulungu, kapena kugwirizana ndi cifuniro cace, mtima umadzazidwa ndi kukaika; ndipo m’kuphunzira Bible mumaturukanso kusakhulupirira. Mdaniyo amalamulira maganizo, ndipo amatiuza matanthauzo amene sali abwino. Pamene anthu sali kufuna kugwirizana ndi Mulungu m’mau ndi m’nchito zawo, pompo, ngakhale ali ophunzira kwambiri, adzacimwa pozindikira malembo, ndipo si kuli kwabwino kukhulupirira mafotokozo awo. Iwo amene ayang’ana malembo kupezamo zosiyana alibe maso a uzimu. Ndi masomphenya okhota adzaona zinthu zambiri zokaikitsa ndi kusakhulupirira m’zinthu zimene ziri zomveka bwino ndi zofewa.MOK 80.3

  Ngakhale acite cizimiza mphoyo, cifukwa ceni ceni ca ku- kaika ndi kusakhulupirira, ndico cikondi ca zoipa. Maphunzitso ndi malangizo a Mau a Mulungu sali abwino kwa mtima wonyada ndi wokonda zoipa, ndipo amene sali olola kumvera zofunsa zace ali ofulumira kukaika za ulamuliro wace. Ngati tifuna kucifika coonadi, tidzikhala ndi cifuniro coona kudziwa coonadi, ndi mtima wolola kucimvera. Iwo amene aphunzira Bible ndi mzimu wotere, adzapeza umboni wocuruka kut. i ali Mau a Mulungu, ndipo adzapeza cizindikiritso ca coonadi cimene cidzawapatsa iwo nzeru kufikira cipulumutso.MOK 80.4

  Kristu anati, “Ngati munthu ali yense afuna kucita cifuniro cace, adzazindikira za ciphunzitsoco.” (Yohane 7: 17. ) M’malo mwa kufunsa ndi kupeza zifukwa ndi zimene suzimvetsetsa, samalira kuwala kumene walandira kale, ndipo udzalandira kuwala kocuruka. Ndi cisomo ca Kristu, cita nchito iri yonse imene uli kuizindikira, ndipo udzakhoza kuzindikira ndi kucita zimene uli kuzikaika tsopano.MOK 81.1

  Ulipo umboni umene uli wotseguka kwa onse, — ophunziritsa, ndi osaphunzira konse, — ndiwo umboni wa macitidwe. Mulungu atiitana ife kuti tiyese tokha kuonadi kwa Mau ace, ndi coonadi ca malonjezano ace. Iye atiuza ife, “Talawani, ndipo muone kuti Yehova ndiye wabwino.” (Salmo 34: 8. ) M’malo mwa kutsa mira pa mau a munthu wina, tilawe tokha. Iye ati, “Pempham, ndipo mudzalandira.” (Yohane 16: 24. ) Malonjezano ace adzakwanitsidwa. Sanalephere ndi kale lonse; ndipo sangalephere konse. Ndipo pamene ife tiri kuyandikira kwa Yesu, ndi kukondwera m’cidzalo ca cikondi cace, kukaika kwathu ndi mdima zidzakanganuka cifukwa ca kuwala kwa nkhope yace.MOK 81.2

  Mtumwi Paulo ati kuti Mulungu “anatilanditsa ife ku ulamuliro wa mdima, natisunthitsa kutilowetsa m’ufumu wa Mwana wa cikondi cace.” (Akolose 1: 13. ) Ndipo ali yense amene wapitirira kucokera ku imfa kunka ku moyo, ali wokhoza kuikapo cizindikiro cace kuti Mulungu ali woona.” (Yohane 3: 33. ) Angathe kucitira umboni, “Ndinasowa cithangato, ndipo ndinacipeza mwa Yesu. Cosowa ciri conse cinapatsidwa, njala ya mtima wanga inakwanitsidwa; ndipo tsopano kwa ine Bible ali bvumbulutso la Yesu Kristu. Kodi uli kufunsa cifukwa ciani ndimakhulupirira mwa Yesu? —Cifukwa kwa ine ali Mpulumutsi wa kumwamba. Cifukwa ciani ndimakhulupira Bible? — Cifukwa ndapeza kuti ndiwo mau a Mulungu kwa moyo wanga.” Tidzakhala nawo umboni mwa ife tokha kuti Bible ali woona, kuti Kristu ali Mwana wa Mulungu. Ife tidziwa kuti sitiri kutsata miyambi yocenjerera.MOK 81.3

  Petro adandaulira abale ace kuti “akule m’cisomo, ndi m’ cidziwitso ca Ambuye wathu ndi Mpulumutsi Yesu Kristu.” (2 Petro 3: 18. ) Pamene anthu a Mulungu ali kukula m’cisomo, adzalandira kosaleka cizindikiritso ca Mau ace. Adzazindikira kuwala kwatsopano ndi ubwino m’coonadi copatulika. Zimenezi zinali zoonadi m’mwambi wa mpingo m’mibadwo yonse, ndipo zidzacitikabe comweco kufikira cimaliziro. “Koma mayendedwe a olungama akunga kuunika kwa mbanda kuca, kunkabe kuwala kufikira usana woti mbe.” (Miyambo 4: 18. )MOK 82.1

  Ndi cikhulupiriro tidzaona za mtsogolo, ndi kugwira mapangano a Mulungu a kukula kwa nzeru zathu, mphamvu za munthu kugwirizana ndi za Mulungu, ndi mphamvu zamoyo uli wonse kugwirizana ndi Kasupe wa kuunika. Tidzakondwera kuti zonse zimene zinali kutibvuta m’macitidwe a Mulungu zidzakhala zomveka; zinthu zobvuta kumva zidzafotokozedwa. Ndipo kumene mitima yathu inali kupeza cisokonekero ndi zosagwirizana. tidzaona kugwirizana kwangwiro ndi kwabwino. “Pakuti tsopano tipenya m’kalilore, ngati cimbuuzi; koma pomwepo maso ndi maso: tsopano ndizindikira mdera mdera; koma pomwepo ndidzazindikiratu monganso ndazindikiridwa.” (1 Akor. 13: 12. )MOK 82.2

  Larger font
  Smaller font
  Copy
  Print
  Contents