Loading...
Larger font
Smaller font
Copy
Print
Contents
  • Results
  • Related
  • Featured
No results found for: "".
  • Weighted Relevancy
  • Content Sequence
  • Relevancy
  • Earliest First
  • Latest First
    Larger font
    Smaller font
    Copy
    Print
    Contents

    MUTU 10—KUDZIWA MULUNGU

    Mulungu ali kufuna kudziululira kwa ife ndi kutiyanjanitsa ife ndi Iye m’njira zambiri. Cilengedwe ciri kulankhula nafe osaleka. Mtima wotseguka udzatsimikizidwa ndi cikondi ndi ulemerero wa Mulungu woonekera mu nchito ya manja ace. Khutu lomvetsera lingathe kumva ndi kuzindikira zonena za Mulungu kupyolera mwa zinthu za cilengedwe. Minda yobiriwira, mitengo yaitari, mphundu ndi maluwa, mitambo, mvula, mtsinje woyenda, ulemerero wa kumwamba, zimalankhula ndi mitima yathu, ndi kutiitana ife kuti tizolowerane ndi Iye amene adalenga zonsezo.MOK 63.1

    Mpulumutsi wathu anamanga maphunziro ace a mtengo wapatari ndi zinthu za cilengedwe. Mitengo, mbalame, maluwa a m’madambo, mapiri, nyanja, ndi miyamba yabwino, pamodzi ndi zooneka ndi zocitika m’moyo wa tsiku liri lonse, zonsezi zinalumikidwa ndi mau a coonadi, kuti maphunziro ace adzikumbukiridwa, ngakhale pakati pa zinchito za moyo wa munthu.MOK 63.2

    Mulungu afuna ana ace kuti adzizindikira nchito zace, ndi kukondwera ndi zokoma za cete zimene Iye anakometsa nazo kwathu kwa dziko lapansi. Iye amakonda zinthu zokometsera, ndipo koposa zokometsera za kunja amakondetsa zokometsera za makhalidwe; Iye afuna kuti ife tikhale angwiro ndi osalala monga maluwa.MOK 63.3

    Ngati tingamvetsere, nchito zolengedwa za Mulungu, zidzatiphunzitsa ife maphunziro abwino a kumvera ndi cikhulupiriro. Kuyambira nyenyezi zimene zimangoyendabe m’njira zawo zopanda mkwaso mlengalenga ku mibadwo mibadwo, kufikira kanthu kocepetsetsa ka pa dziko lapansi, zinthu za cilengedwe zimamvera cifuniro ca Mlengi wawo. Ndipo Mulungu amasamalira kanthu kali konse, ndi kuthangata kanthu kali konse kamene Iye adakalenga. Iye amene amanyamula maiko osawerengeka m’cilengedwe cace conse, pa nthawi yomweyo amasamalira zosowa za katimba kakang’ono, kamene kamayimba nyimbo yace wopanda mantha. Pamene anthu apita ku nchito zawo za masiku onse ndi pamene ali kupemphera; pamene ali kugona usiku, ndi pamene adzuka m’mawa; pamene munthu wolemera ali kudya phwando m’cinyumba cace, kapena pamene wosauka asonkhanitsa ana ace kudya topanda pace, ali yense wa iwo amayang’ani - dwa ndi Atate wa kumwamba. Palibe misozi imene imagwa yosadziwika ndi Mulungu. Palibe cimwemwe cimene Iye sacidziwa.MOK 63.4

    Ngati tingakhulupirire ndithu izi, nkhawa zonse zidzacoka. Miyoyo yathu sidzagwiritsidwa mwala monga iri tsopano; cifukwa cinthu ciri conse cacikuru kapena cacing’ono, cidzasiyidwa m’manja a Mulungu, amene sabvutika ndi kucuruka kwa zosamalira, kapena kutopa ndi kulemera kwao. Pompo tidzakhala ndi mtendere wa mu mtima umene ambiri saudziwa.MOK 64.1

    Pamene mtima wako ukondwera ndi zinthu zokongola za dziko lapansi, ganiza za dziko lirinkudza limene silidzadziwa zowawa za ucimo ndi imfa; kumene nkhope ya cilengedwe sidzabvalanso mthunzi wa temberero. Mtima wako uganize za kwawo kwa opulumutsidwa, ndi kukumbukira kuti kudzakhala kokometsetsa koposa m’mene uganiziramo. Mu mphatso zosiyana za Mulungu mwa cilengedwe timaonamo mwa cimbuuzi ulemerero wa Mulungu. Kwalembedwa. “Zimene diso silinaziona, ndi khutu silinazimva, nisizinalowa mu mtima wa munthu, zimene ziri zonse Mulungu anakonzeratu iwo akumkonda Iye.” (1 Akor. 2: 9. )MOK 64.2

    Wolemba Poetry ndi wophunzira za cilengedwe amanena zambiri za cilengedwe, koma Mkristu ndiye amakondwera nako kukoma kwa dziko ndi ciyamiko cacikuru, cifukwa iye amazindikira nchito ya Atate wace, naona cikondi cace m’duwa ndi citsamba ndi mtengo. Palibe wina angazindikire kukongola kwa phiri ndi dambo, mtsinje ndi nyanja, amene samaziyang’ana izo kuti ziri citsimikizo ca cikondi ca Mulungu kwa anthu.MOK 64.3

    Mulungu amalankhula nafe kupyolera mwa nchito zace za cilengedwe, ndi kupyolera mu mphamvu ya Mzimu wace mu mtima. Mwa zinthu zotizungulira, ndi mwa zinthu zooneka tsiku ndi tsiku, tingapezemo maphunziro abwino, ngati mitima yathu iri yotseguka kuzizindikira. Davide, pofotokoza nchito ya ukuru wa Mulungu ati, “Dziko lapansi ladzala ndi cifundo ca Yehova.” (Salmo 33: 5. ) “Wokhala nazo nzeru asamalire izi, ndipo azindikire za cifundo za Yehova.” (Salmo 107: 43. )MOK 64.4

    Mulungu amalankhula kwa ife M’mau ace. M’menemo muli bvumbulutso langwiro la makhalidwe ace, za macitidwe ace ndi anthu, ndi za nchito yaikuru ya ciombolo. M’menemo muli mwambi wa akulu a kale ndi aneneri ndi wa anthu ena oyera mtima akale. Iwo anali anthu “akumva zomwezi tizimva ife.” (Yakobo 5: 17. ) Ife tiona m’mene iwo anali kulimbana ndi zogwetsa mphwai monga ife tomwe, m’mene iwo anagwera m’mayeso monga timagwa ife, koma nalimbanso mtima nagonjetsa ndi cisomo ca Mulungu: ndipo popenyerera, ifenso tilimbika mtima mu nkhondo yathu ya cilungamo. Pamene tiwerenga za macitidwe abwino opatsidwa kwa iwo, za kuunika ndi cikondi ndi madalitso amene anali kukondwera nawo, ndi nchito imene adacita mwa cisomo copatsidwa kwa iwo, mzimu umene unawauzira iwo, umayatsanso moto wa kupambanitsa m’mitima yathu, ndi cifuniro ca kufanana nawo m’makhalidwe, — kufanana nawo pa kuyenda ndi Mulungu.MOK 64.5

    Yesu anati za Malembo a Cipangano Cakale, — koposa kotani nanga Malembo a Cipangano Catsopano, —“Ndipo akundicitira Ine umboni ndi iwo omwewo” (Yohane 5: 39), Mombolo wathu, mwa Iye amene muli ciyembekezo cathu ca moyo wosatha. Inde, Bible lonse lifotokoza za Kristu. Kuyambira mau oyamba a cilengedwe, — cifukwa “kanthu kali konse kanapangidwa sikanapangidwa kopanda Iye” (Yohane 1: 3), — kufikira ku lonjezo lotsiriza, “Taona ndidza msanga” (Cibvu. 22: 12), tiri kuwerengamo za nchito zace ndi kumvetsera mau ace. Ngati ufuna kuzolowerana ndi Mpulumutsi, phunzira Malembo Opatulika.MOK 65.1

    Dzaza mtima wonse ndi mau a Mulungu. Iwo ali madzi a moyo, akuziziritsa ludzu lako. Iwo ali mkate wa moyo wocokera kumwamba. Yesu ati, “Ngati simukudya thupi la Mwana wa munthu, mulibe moyo mwa inu nokha.” Ndipo anafotokoza za Iye yekha pa kunena, “Mau amene ndalankhula ndi inu ndiwo Mzimu, ndiponso moyo.” (Yohane 6: 53, 63. ) Matupi athu amapangidwa ndi zimene tidya ndi kumwa; ndipo monga m’thupi moteronso mu mzimu: timapatsa mphamvu ku moyo wathu wa uzimu ndi zimene timaganiza.MOK 65.2

    Mutu wa ciombolo ndiwo umene angclo alakalaka kuonamo; idzakhala nkhani ndi nyimbo ya oomboledwa ku nthawi zonse zosatha. Kodi sitiyenera kuciganizira ndi kuciphunzira tsopano? Cifundo ndi cikondi cosatha ca Yesu, nsembe imene anaipereka cifukwa ca ife, tiyenera kuziganizira ndi mitima ya cisoni ndi yotsimikiza. Tiyenera kuganizira za makhalidwe a Mombolo wathu wokondedwa ndi Wotipembedzera ife. Tiyenera kuganizira za nchito ya Iye amene anadza kupulumutsa anthu ace ku macimo awo. Tikamaganiza cotero zinthu za kumwamba, cikhulupiriro cathu ndi cikondi cathu cidzakula ndi mphamvu, ndipo mapemphero athu adzalandirika kwa Mulungu, cifukwa adzasanganikira kwambiri ndi cikhulupiriro ndi cikondi. Iwo adzakhala olongosoka ndi otentha. Mu mtima mudzakhala cikhulupiriro cosalekeza ca mwa Yesu, ndi macitidwe a moyo a masiku onse mu mphamvu yace ya kupulumutsa konse konse iwo akuyandikira kwa Mulungu mwa Iye.MOK 65.3

    Pamene tilingirira za ungwiro wa Mpulumutsi, tidzalakalaka kusinthidwa konse konse, ndi kukonzedwanso m’cifanizo ca ungwiro wace. Moyo udzamva njara ndi ludzu la kufuna kukhala ofanana ndi Iye amene timpembedza. Maganizo athu akamaganiza kwambiri za Kristu, tidzalankhulanso kwambiri za Iye kwa anzathu, ndi kumuonetsera Iye ku dziko lapansi.MOK 66.1

    Bible sanalembedwa kwa ophunziritsa okha; koma makamaka analembedwa kwa anthu wamba. Zoonadi zazikuru zoyenera cipulumutso ca anthu zinalembedwa mooneka bwino monga usana; ndipo palibe angaphophonye ndi kusocera koma iwo amene atsata cifuniro cawo m’malo mwa kutsata cifuniro coonetsedwa bwino lomwe ca Mulungu.MOK 66.2

    Tisamalandira umboni wa munthu kutiuza zimene malembo aphunzitsa, koma tidziphunzira tokha mau a Mulungu. Ngati tingamangolandira maganizo a anzathu, cangu cathu ndi nzeru zathu zidzacepa. Mphamvu za malingaliro zidzacepa cifukwa ca kusacita nawo pa kuganiza zinthu za Mulungu, ndipo tidzataya nzeru zathu za kuzindikira matanthauzo akuya a Mau a Mulungu. Malingaliro adzakula ngati ticita navvo kuphunzira kugwirizana kwa maphunzitso a Bible, kulinganiza lembo ndi lembo, ndi zinthu za uzimu ndi za uzimu.MOK 66.3

    Palibe kanthu kenanso kangathe kulimbitsa malingaliro athu koposa kuphunzira malembo a Bible. Palibe bukhu lina la mphamvu kuutsa maganizo ndi kuwapatsa mphamvu, monga zoonadi za Bible. Anthu akadaphunzira mau a Mulungu monga ayenera, akadakhala ndi nzeru zambiri, ndi makhalidwe abwino, ndi nchito yokhazikika imene sionekaoneka masiku ano.MOK 66.4

    Kuwerenga Bible mofulumira, ungopezamo kaubwino pang’ono. Munthu angathe kuwerenga Bible lonse, koma nalephera kuona kukoma kwace kapena kuzindikira matanthauzo ace akuya obisika. Vesi limodzi litaphunziridwa bwino kufikira matanthauzo ace amveka mu mtima, ndi kuona kugwirizana kwace ndi nzeru ya cipulumutso, liri la mtengo wapatari, koposa kuwerenga macaputara ambiri osapindulamo kanthu kothangata mtima. Sunga Bible wako. Ukapeza nthawi muwerenge; loweza malembo ace. Ngakhale uli kuyenda mu mseu, ungawerenge vesi, ndi kuliganizira, potero lidzakhazikika mu mtima mwako.MOK 66.5

    Sitingathe kulandira nzeru opanda kuyang’anitsitsa koona ndi kuphunzira pamodzi ndi pemphero. Mbali zina za Malembo ziri zofewa kwambiri inde kuti munthu ali yense angathe kumvetsetsa mofewa; koma ziripo mbali zina, zimene matanthauzo awo sali pamwamba, pooneka msanga. Lembo liyenera kulinganizidwa ndi lembo linzace. Tiyenera kufunafuna mosamalira, ndi kuganiza uli kupemphera mu mtima. Kuphunzira kotere kudzabwezeredwa mphotho koposa. Monga wa mumgodi amapeza cuma cobisika pansi pa dziko, cotero iye amene, mwa khama, afunafuna Mau a Mulungu monga cuma cobisika, adzapeza zoonadi za mtengo wapatari, zimene ziri zobisika kwa iye amene afuna mwa mphwayi. Mau a Mulungu, atakhala mu mtima, adzakhala monga mitsinje yotumphuka kucokera ku kasupe wa moyo.MOK 66.6

    Usamaphunzira Bible wopanda pemphero. Tisanalitsegule, tiyenera kupempha kuwala kwa Mzimu Woyera, ndipo kudzapatsidwa. Pamene Natanieli anadza kwa Yesu, Mpulumutsi ananena, “Ona mu Israyeli ndithu, mwa iye mulibe cinyengo!” Natanieli anati, “Kucokera kuti mundidziwa ine?” Yesu anayankha, “Asanakuitane Filipo, pokhala iwe pansi pa mkuyu, ndinakuona iwe.” (Yohane 1: 47, 48. ) Ndipo Yesu adzationa ifenso m’malo a mtseri a pemphero, ngati tingampemphe kuunika, kuti tidziwe cimene ciri coonadi. Angelo a ku dziko lowala, adzakhala ndi iwo amene mu mtima mwawo afuna kutsogozedwa ndi Mulungu.MOK 67.1

    Mzimu Woyera umakuza ndi kulemekeza Mpulumutsi. Nchito yace ndiyo kuonetsera Kristu, ungwiro wa cilungamo cace, ndi cipulumutso cacikuru cimene tiri naco mwa Iye. Yesu ati, “Iyeyo adzatenga za mwa Ine nadzalalikira kwa inu.” (Yohane 16: 14. ) Mzimu wa coonadi ndiye mphunzitsi wa luso wa coonadi. Mulungu amalemekeza mtundu wa anthu, popeza anapereka Mwana wace kuwafera iwo, ndi kupereka Mzimu wace kukhala mphunzitsi ndi mtsogoleri wawo kosalekeza.MOK 67.2

    Larger font
    Smaller font
    Copy
    Print
    Contents