Loading...
Larger font
Smaller font
Copy
Print
Contents
 • Results
 • Related
 • Featured
No results found for: "".
 • Weighted Relevancy
 • Content Sequence
 • Relevancy
 • Earliest First
 • Latest First
  Larger font
  Smaller font
  Copy
  Print
  Contents

  MUTU 1—CIKONDI CA MULUNGU KWA MUNTHU

  Cilengedwe ndi cibvumbulutso zimacitira umboni za cikondi ca Mulungu. Atate wathu wa kumwamba ndi kasupe wa moyo, wa nzeru, wa cimwemwe. Taonani zinthu zozizwitsa zokometsetsa za cilengedwe. Taganizani za nchito zace zozizwitsa pa kukwanitsa zosowa ndi cikondwerero ca anthu ndi ca zolengedwa zonse. Dzuwa ndi mvula, zimene zimakondweretsa ndi kutsitsimutsa dziko, mapiri ndi nyanja ndi madambo, zonsezi zimatiuza ife za cikondi ca Mlengi. Amene amakwanitsa zosowa za zolengedwa zace ndiye Mulungu. Davide ananena mau okometsetsa otere, —MOK 7.1

  “Maso a onse ayembekeza Inu ndipo muwapatsa cakudya cawo m’nyengo zawo. Muolowetsa dzanja lanu, nimukwaniritsira za moyo zonse cokhumba cawo.” Salmo 145: 15, 16.MOK 7.2

  Mulungu anapanga munthu woyera mtima ndi wokondwa; ndipo dziko lokongola pamene linaturuka m’manja a Mlengi linalibe kadontho kobvunda kapena mthunzi wa temberero. Cimene cadzetsa tsoka ndi imfayi, ndi kuswa malamulo a Mulungu — malamulo a cikondi. Komabe ngakhale pakati pa zobvuta zimene zimadza cifukwa ca zoipa, cikondi ca Mulungu cimaonekera. Zidalembedwa kuti Mulungu anatemberera nthaka cifukwa ca munthu. (Gen. 3: 17. ) Minga ndi mitula— mabvuto ndi mayeso, zimene zimacititsa moyo wace kukhala wa nchito ndi wa nkhawa — zinaperekedwa cifukwa ca ubwino wace, kuti zikhale za kumphunzitsa nzeru ya Mulungu ya kumtukula ku cionongeko ndi manyazi amene anadza ndi ucimo. Ngakhale dziko lidagwa si la cisoni cokha cokha. Mwa cilengedwe muli uthenga wa ciyembekezo ndi cisangalatso. Pa mitengo ya minga pali maluwa.MOK 7.3

  Mau akuti “Mulungu ali cikondi,” alembedwa pa duwa liri lonse, ndi pa udzu uli wonse. Mbalame zimayimba nyimbo mokondwa mlengalenga, maluwa onunkhira, mitengo yobiriwira ya m’nkhalango, — zonse zimacitira umboni cisamaliro ca Atate Mulungu wathu ndi kuti Iye amafuna kukondwetsa ana ace.MOK 7.4

  Mau a Mulungu amaonetsa makhalidwe ace. Iye mwini ananena za cikondi cace ndi cifundo cace. Pamene Mose anapemphera, “Ndionetsenitu ulemerero wanu,” Yehova anayankha, “Ndidzapititsa ukoma wanga wonse pa maso pako.” (Eksodo 33: 18, 19. ) Uwu hdiwo ulemerero wace. Yehova anapita pa maso ya Mose, napfuula, “Yehova, Yehova, Mulungu wa cifundo ndi wa cisomo, wolekereza, ndi wa ukoma mtima wocuruka, ndi wa coonadi; wa kusungira anthu osawerengeka cifundo, wakukhululukira mphulupulu ndi kulakwa ndi kucimwa.” (Eksodo 34: 6, 7. ) Iye “sasunga mkwiyo wace ku nthawi yonse popeza akondwera naco cifundo.” (Mika 7: 18. ) “Ndi woleka coipaco.” (Yona 4: 2. )MOK 7.5

  Mulungu anamangirira mitima yathu kwa Iye ndi zizindikiro zosawerengeka m’mwamba ndi m’dziko lapansi. Mulungu anafuna kudziululira kwa ife kupyolera mwa nsinga za cilengedwe, zimene ziri nsinga zolimba za cikondi za dziko lapansi zimene mitima ya anthu ingazidziwe. Koma ngakhale zimenezi sizimaonetsera kweni kweni za cikondi cace. Ngakhale mboni zonsezi zinaperekedwa, mdani wa zabwino anadetsa mitima ya anthu kotero kuti anali kuyang’ana Mulungu ndi mantha; anamuganizira ngati woopsa wosakhululukira. Satana anatsogolera anthu kuganiza kuti Mulungu ali woweruza wa nkharwe, —amene zocita zace zonse ziri za ukari. Iye anamuganizira Mulungu ngati wakungoyang’anira ndi diso la nsanje kulonda zolakwa ndi zophophonya za anthu, kuti awalange. Yesu anadza kudzakhala pakati pa anthu kudzacotsa mdima umenewu pakusonyeza ku dziko lonse cikondi cosatha ca Mulungu.MOK 8.1

  Mwana wa Mulungu anadza kucokera kumwamba kudzaonetsera Atate. “Palibe munthu anaona Mulungu nthawi zonse; Mwana Wobadwa yekha wakukhala pa cifuwa ca Atate, Iyeyu anafotokozera.” (Yohane 1: 18. ) “Ndipo palibe wina adziwa Atate, koma Mwana yekha, ndi iye amene Mwana afuna kumuululira.” (Mateyu 11: 27. ) Pamene mmodzi wa akuphunzira anafunsa, “Tionetsereni Atate,” Yesu anayankha, “Kodi ndiri ndi inu nthawi yaikuru yotere, ndipo sunandizindikira Filipo? Iye amene wandiona Ine waona Atate, unena iwe bwanji, Mutionetsere Atate?” (Yohane 14: 8, 9. ) MOK 8.2

  Pakufotokoza za nchito yace ya dziko lapansi, Yesu anati, “Iye anandidzoza Ine ndiuze anthu osauka Uthenga Wabwino, anandituma Ine kulalikira amnsinga mamasulidwe, ndi akhungu kuti apenyenso, kuturutsa ndi ufulu wophwanyika.” (Luka 4: 18. ) Imeneyi ndiyo inali nchito yace. Iye anapitapita nacita zabwino, ndi kuciritsa onse osautsidwa ndi Satana. Inalipo midzi yina yathunthu imene kubuula kwa odwala sikunali kumvekamo m’nyumba iri yonse; cifukwa Iye anapita pakati pawo, naciritsa odwala awo onse. Nchito yaceyo inali umboni wakuti anadzozedwa ndi Mulungu. Cikondi ndi cifundo zinaonetsedwa m’nchito iri yonse ya moyo wace; mtima wace unali kuwamvera cifundo ana a anthu. Iye anatenga makhalidwe a munthu, kuti akwanitse zosowa za munthu. Osauka ndi onyozeka sanali kuopa kudza kwa Iye. Ngakhale tiana tinadza kwa Iye. Tinakonda kukwera pa maondo pace, ndi kuyanga’nitsa nkhope yace, yodzazidwa ndi cikondi.MOK 8.3

  Yesu sanasiye mau amodzi a coonadi, koma masiku onse anali kuwalankhula m’cikondi. Polankhulana ndi anthu Iye anacita ndi luso ndi moganiza ndi mokoma mtima. Sanali wacipongwe, sanalankhule mau aukari, ndipo sanapweteke mtima wa munthu ali yense. Sanapeze cifukwa ndi zofooka za anthu. Iye analankhula coonadi, koma masiku onse analankhula mwa cikondi. Iye anadzudzula cinyengo, kusakhulupirira, ndi mphulupulu; koma misozi inali m’maso mwace pamene anali kunena mau odzudzulawo. Iye analirira Yerusalemu, mzinda umene anaukonda, umene unakana kumlandira Iye, amene ali Njira ndi Coonadi, ndi Moyo. Iwo anakana Mpulumutsi wawo, koma Iye anawamvera cifundo. Moyo wace unali wakudzikaniza yekha, ndi woganiza za kusamalira ena. Moyo wa munthu ali yense unali wa mtengo wapatali pa maso pace. Ngakhale anali nawo makhalidwe oyera a Umulungu, Iye anali kusamalira munthu ali yense wa banja la Mulungu. Mwa anthu onse Iye anaona miyoyo yakugwa imene anadzera kuipulumutsa.MOK 9.1

  Oterewa ndiwo makhalidwe a Kristu amene anaonekera m’moyo mwace. Amenewa ndiwo makhalidwe a Mulungu. Mitsinje ya cifundo coonetsedwa mwa Kristu, imadza kwa ana a anthu kucokera mu mtima mwa Atate. Yesu, Mpulumutsi wa cifundo ndi wokoma mtima, “Anaonetsera Mulungu m’thupi lace.” (1 Tim. 3: 16. )MOK 9.2

  Yesu anakhala pansi pano nasautsidwa, nafa cifukwa ca kutiombola ife. Iye anasanduka “Munthu wa zisoni,” kuti ife tikalandirane nawo cimwemwe cosatha. Mulungu analola Mwana wace wokondedwa, wodzazidwa ndi cisomo ndi coonadi, kucoka ku dziko la ulemerero wosaneneka, kudza ku dziko loipitsidwa ndi ucimo, lodetsedwa ndi mthunzi wa imfa ndi temberero. Iye anamlola kusiya Atate wace wokonda, ndi cilemekezo ca angelo, kudzamva manyazi, kudzacitidwa cipongwe, ndi kunyozedwa, ndi kudanidwa, ndi imfa. “Cilango cotitengera ife mtendere cinamgwera Iye; ndipo ndi mikwingwirima yace ife taciritsidwa.” (Yesaya 53: 5. ) Muyang’aneni Iye m’cipululu, m’Getsemane pa Mtanda! Mwana wa Mulungu wopanda cirema anasenza katundu wa zoipa. Iye amene anali mmodzi ndi Mulungu, anamva m’moyo mwace kulekanitsidwa koopsa kumene kumacitika ndi zoipa pakati pa Mulungu ndi munthu. Zimenezi zidamliritsa mwa cisoni, “Mulungu Wanga, Mulungu Wanga, mwandisiiranjx Ine?” (Mateyu 27: 46. ) Cimene cinaswa mtima wa Mwana wa Mulungu, ndi katundu wa zoipa, pa kuzindikira kuopsa kwace, ndi kulekanitsidwa kwace kwa moyo ndi Mulungu.MOK 9.3

  Koma nsembe yaikuruyi sinapangidwe cifukwa cofuna kulenga mu mtima mwa Atate cikondi pa munthu, kapena kumpangitsa kulola kupulumutsa. Iai konse! “Mulungu anakonda dziko lapansi kotero kuti anapatsa Mwana wace wobadwa yekha.” (Yohane 3: 16. ) Atate atikonda ife si cifukwa ca nsembe yaikuruyo, koma Iye anatipatsa ife nsembeyo, cifukwa ca kutikonda ife. Kristu anali Mnkhoswe, kupyolera mwa Iyeyo anali kutsanulira cikondi cace cosatha pa dziko lolepherali. “Mulungu anali mwa Kristu ali kuyanjanitsa dziko kwa Iye yekha.” (2 Akor. 5: 19. ) Mulungu anasautsidwa pamodzi ndi Mwana wace. M’kusautsidwa kwa ku Getsemane, imfa ya pa Golgota, mtima wa cikondi wa Mulungu unalipira mtengo wa ciombolo cathu.MOK 10.1

  Yesu anati, “Cifukwa ca ici Atate andikonda Ine, cifukwa nditaya Ine moyo wanga, kuti ndikautengenso.” (Yohane 10: 17. ) Ndiko kuti, “Atate wanga akukondani inu kotero kuti anandikonda Ine koposa cifukwa ndinapereka moyo wanga kukuombolani inu. Pakusanduka wolowa m’malo mwanu ndi Cikole canu; pa kupereka moyo wanga, pa kutenga mangawa anu, ndi macimo anu, ndikondedwa ndi Atate wanga; cifukwa ndi nsembe yanga, Mulungu angathe kukhala wolungama, ndi womuyesera wolungama iye amene akhulupirira Yesu.”MOK 10.2

  Palibe wina angathe kutiombola koma Yesu yekha; pakuti Iye yekha amene anali pa cifuwa ca Atate ndiye angathe kufotokoza za Iye. Iye yekha amene amadziwa kuya ndi utari wa cikondi ca Mulungu, ndiye angathe kucionetsera. Palibenso kena koposa nsembe imene Kristu anaicita cifukwa ca anthu olephera, kangathe kutsimikiza cikondi ca Atate kwa anthu otaika.MOK 10.3

  “Mulungu anakonda dziko lapansi kotero kuti anapatsa Mwana wace wobadwa yekha.” Sanangompereka kudzakhala pakati pa anthu pokha, kunyamula zoipa zawo, ndi kufera nsembe yawo, koma anampereka kwa mtundu wonse wotaika. Kristu anadzilinganiza yekha ndi zokondweretsa ndi zosowa za anthu. Iye amene anali mmodzi ndi Mulungu anadzilumikiza ndi ana a anthu ndi mfundo zosaduka. Yesu, “sacita manyazi kuwachula iwo abale.” (Ahebri 2: 11. ) Iye ndiye nsembe yathu, Mnkhoswe wathu, Mbale wathu, wakunyamula makhalidwe athu a umunthu patsogolo pa mpando wacifumu wa Atate, ndipo ku- pyolera zaka zosatha adzakhala mmodzi wa mtundu umene anaupulumutsa, — nadzachedwabe Mwana wa munthu. Zonsezi zinacitika kuti munthu akhululukidwe ku cionongeko ca ucimo, kuti aonetsere cikondi ca Mulungu, ndi kugawana nawo cimwemwe copatulika.MOK 10.4

  Mtengo umene unaperekedwa kutiombola ife, nsembe yosatha ya Atate wathu wa kumwamba pakupereka Mwana wace kudzatifera ife, ziyenera kutipatsa maganizo akuru a cimene tidzakhala kupyolera mwa Kristu. Pamene mtumwi Yohane, wogwidwa ndi Mzimu Woyera anaona utari, kuya, bwambi wa cikondi ca Atate kwa mtundu woonongeka, anadzazidwa ndi kupembedza ndi kulemekeza; ndipo, polephera kupeza cinenero cokwamira kufotokoza kukula kwa cikondi cimeneci iye anauza dziko lonse kuciyang’ana. “Taonani cikondico Atate ali naco pa ife, kuti tichedwe ana a Mulungu.” (1 Yohane 3: 1. ) Zimenezi zimuyesera munthu kukhala wa mtengo wa patari! Cifukwa ca kuswa malamulo ana a anthu anasanduka akapolo a Satana. Ndi cikhulupiriro mu nsembe ya Kristu ana a Adamu adzasanduka ana a Mulungu. Pakutenga makhalidwe a umunthu, Kristu anatukula anthu. Kupyolera mwa Kristu anthu olephera adzaikidwa kumene adzakhaladi oyenera kuchedwa “ana a Mulungu.”MOK 11.1

  Cikondi cotere ncosayerekezeka. Ana a Mfumu ya kumwamba! Lonjezo loposa! Cinthu coyenera kuciganizira! Cikondi cosayerekezeka ca Mulungu kwa dziko limene silinamkonde Iye! Ganizo limeneli liri ndi mphamvu yotyola moyo, ndi kupangitsa mtima kugonjera cifuniro ca Mulungu. Tikamaphunzira kwambiri makhalidwe a Mulungu m’kuwala kwa mtanda, tidzaonanso kwambiri cifundo, nsisi, ndi cikhululukiro zitalumikizana ndi ubwino ndi ciweruzo, ndipo tidzazindikiranso koposa maumboni osawerengeka a cikondi cosatha, ndi cifundo copitirira cifundo ca mai kwa mwana wace wa mphulupulu.MOK 11.2

  Larger font
  Smaller font
  Copy
  Print
  Contents