Loading...
Larger font
Smaller font
Copy
Print
Contents
  • Results
  • Related
  • Featured
No results found for: "".
  • Weighted Relevancy
  • Content Sequence
  • Relevancy
  • Earliest First
  • Latest First
    Larger font
    Smaller font
    Copy
    Print
    Contents

    MUTU 6—CIKHULUPIRIRO NDI KULANDIRIDWA

    PAMENE cikumbumtima cako cadzutsidwa ndi Mzimu Woyera, waona kuipa kwa ucimo, mphamvu yace, kutsutsidwa kwace, tsoka lace; ndipo umauyang’ana ndi kunyansidwa nawo. Umadziwa kuti ucimo udakulekanitsa ndi Mulungu, kuti uli mu ukapolo wa zoipa. M’mene uli kulimbika kudzipulumutsa wekha, momwemo udzazindikira kuti ulibe mphamvu ya kudzithangata wekha. Maganizo ako ali osayera, mtima wako uli wonyansa. Iwe uona kuti mtima wako unadzazidwa ndi kudzikonda wekha ndi zoipa. Ufuna kukhululukidwa, kutsukidwa, ndi kumasulidwa. Ufuna kuyanjana ndi Mulungu, ndi kufanana naye, — nanga ungacite ciani kulandira zonsezi?MOK 37.1

    Usowa mtendere, — cikhululukiro ca Mulungu, ndi cikondi m’moyo mwako. Sungathe kuzigula ndi ndalama, sungathe kuzipeza ndi nzeru zako; sungayembekeze kuzipeza, ndi kuyesa kwako kokha. Koma Mulungu angokupatsa kwaulere, “opanda ndalama ndi wopanda mtengo.” (Yesaya 55: 1. ) Zonsezi zidzakhala zako ngati ungangotambasula manja ako ndi kuzilandira. Yehova ati, “Ngakhale zoipa zanu ziri zofiira, zidzayera ngati matalala; ngakhale ziri zofiira ngati kapezi zidzakhala ngati ubweya wa nkhosa woti mbu.” (Yesaya 1: 18. ) “Ndipo ndidzakupatsani mtima watsopano, ndi kulonga m’kati mwanu mzimu watsopano.” (Ezek. 36: 26. )MOK 37.2

    Udabvomereza zoipa zako, ndi kuzicotsa mu mtima mwako. Udatsimikiza mtima kudzipereka kwa Mulungu. Tsopano pita kwa Iye, ndi kumpempha kuti atsuke zoipa zako, nakupatse mtima watsopano. Pompo khulupirira kuti adzakucitira izi cifukwa adalonjeza. Limeneli ndilo phunziro limene Yesu anaphunzitsa pamene anali pa dziko lapansi, kuti mphatso imene Mulungu adalonjeza, ife tidzikhulupirira kuti talandira, ndipo idzakhala yathu. Yesu anaciritsa anthu nthenda zawo pamene iwo anali kukhulupirira mphamvu yace; Iye anawathangata m’zinthu zimene anali kuziona, motero anali kumkhulupirira Iye m’zinthu zimene sanali kuziona, — nawatsogolera kukhulupirira mphamvu yace ya kukhululukira zoipa. Izi ananena momveka pa kuciritsa munthu wodwala manjenje: “Koma kuti mudziwe kuti ali nazo mphamvu Mwana wa munthu pansi pano za kukhululukira macimo (pomwepo ananena kwa wodwalayo), Tanyamuka, nutenge chika lako, numuke ku nyumba kwako.” (Mateyu 9: 6. ) Coteronso Yohane mlalikiyo ati, pakunena za zozizwitsa za Yesu, “Koma zalembedwa izi kuti mukakhulupirire kuti Yesu ndiye Kristu Mwana wa Mulungu, ndi kuti pakukhulupirira mukakhale nawo moyo m’dzina lace.” (Yohane 20: 31. )MOK 37.3

    Mu nthano zofewa za m’Bible zofotokoza m’mene Yesu anaciritsira odwala, tingaphunziremo kukhulupirira Iye kwa cikhululukiro ca macimo athu. Tiyeni titaona nthano ya wodwala wa pa Betesda uja. Iye anali wosatha kudzithangata; sanagwire nazo nchito ziwalo zace zaka makumi atatu mphambu zisanu ndi zitatu. Koma Yesu anamuuza iye, “Uka, yalula mphasa yako, nuyende.” Wodwalayo akadafuna akadati, “Ambuye, ngati mungandiciritse ndidzamvera mau anu.” Koma ai, iye anakhulupirira mau a Kristu, anakhulupirira kuti waciritsidwa, ndipo anayesa msanga; iye anafuna kuyenda, ndipo anayendadi. Iye anacita pakumva mau a Kristu, ndipo Mulungu anampatsa mphamvu. Ndipo iye anaciritsidwa.MOK 38.1

    Monga momwemo iwe ndiwe wocimwa. Sungathe kupembedzera zoipa zako zam’mbuyo, sungathe kusintha mtima wako, ndi kudziyeretsa wekha. Koma Mulungu analonjeza kukucitira zonsezi mwa Kristu. Iwe ukhulupirira lonjezanolo. Nubvomereza zoipa zako, ndi kudzipereka kwa Mulungu. Iwe nufuna kumtumikira. Ngati iwe ungacitedi zimenezi, Mulungu adzakwanitsa mau ace kwa iwe. Ngati ukhulupirira lonjezanolo, — khulupirira kuti wakhululukidwa ndi kutsukidwa, — Mulungu adzakucitira; waciritsidwa, monga momwe Kristu anapatsira mphamvu wodwala uja kuyenda pamene anakhulupirira kuti waciritsidwa. Zidzatero ngati iwe ukhulupirira.MOK 38.2

    Usalindire kuti uyambe wamva kuti waciritsidwa, koma nena kuti, “Ndikhulupirira; ndi zoona, sicifukwa ca kuti ndamva, koma cifukwa ca kuti Mulungu adalonjeza.MOK 38.3

    Yesu ati, “Zinthu ziri zonse mukazipemphera ndi kuzipempha, khulupirirani kuti mwazilandira ndipo mudzakhala nazo.” (Marko 11: 24. ) Pali malandiridwe ace a lonjezano limeneli, — kuti tipemphere monga mwa cifuniro ca Mulungu. Koma Mulungu afuna kutitsuka ife mu zoipa zathu, kutiyesa ana ace, ndi kutithangata ife kukhala moyo woyera.MOK 38.4

    Cotero ife tidzipempha madalitso amenewa, ndi kukhulupirira kuti tawalandira, ndi kuthokoza Mulungu kuti tawalandira. Ndi mwai wathu kunka kwa Yesu ndi kukatsukidwa, ndi kuima patsogolo pa malamulo opanda manyazi kapena cisoni. “Cifukwa cace tsopano iwo akukhala mwa Kristu Yesu alibe kutsutsidwa, amene sayenda monga mwa thupi koma monga mwa Mzimu.” (Aroma 8: 1. )MOK 38.5

    Cifukwa cace simuli a inu nokha; mudagulidwa ndi mtengo wapatari. “Podziwa kuti simunaomboledwa ndi zobvunda, golidi ndi siliva,... koma ndi mwazi wa mtengo wace wapatari, monga wa mwana wa nkhosa wopanda cirema ndi wopanda banga.” (1 Pet. 1: 18, 19. ) Ndi nchito ya pafupiyi ya kukhulupirira Mulungu, Mzimu Woyera walenga moyo watsopano mu mtima mwako. Ndiwe monga mwana wobadwa m’banja la Mulungu, ndipo akukonda iwe monga akonda Mwana wace. Popeza wadzipereka kwa Yesu, usabwerere m’mbuyo, usadzicotse kwa Iye, koma tsiku ndi tsiku nena, “Ndine wa Kristu; ndinadzipereka kwa Iye;” ndi kumpempha Iye kukupatsa Mzimu wace, ndi kukusunga ndi cisomo cace. Popeza usanduka mwana wace pakudzipereka kwa Mulungu, ndi kukhulupirira Iye, cotero uyenera kukhala mwa Iye. Mtumwi ati, “Cifukwa cace monga munalandira Kristu Yesu Ambuye, muyende mwa Iye.” (Akolose 2: 6. )MOK 39.1

    Ena amaoneka ngati afuna kuyamba kuyesedwa ndi kudzisonyeza kwa Yehova kuti akonzeka, asanapemphe dalitso lace. Koma ayenera kupempheratu dalitso la Mulungu tsopano lino. Ayenera kulandira cisomo cace, Mzimu wa Kristu, kuwathangata m’zofooka zawo, atapanda kutero sangathe kukaniza zoipa. Yesu akonda kuti ife tidze kwa Iye monga momwe tiri, ocimwa, osowa cithangato, osatha kucita kanthu mwa ife tokha. Tidze ndi zofooka zathu zonse, kupusa kwathu, kucimwa kwathu, ndi kugwa pa mapazi ace ndi kulapa. Ndi ulemerero wace kutifukata m’mikono yace ya cikondi, ndi kumanga mabala athu, ndi kutitsuka ku zoipa zonse.MOK 39.2

    Anthu ambiri amalepherera apa: sakhulupirira kuti Yesu amawakhululukira ali yense pa yekha. Sakhulupirira mau a Mulungu. Iwo amene ayanjana ndi macitidwe ace ayenera kudziwa kuti cikhululukiro ciripo cokwana kwa cimo liri lonse. Cotsani ganizo la kuti malonjezano a Mulungu sali anu. Iwo ali a wocimwa ali yense amene alapa. Mphamvu ndi cisomo kupyolera mwa Kristu zimadza ndi angelo otumikira kwa munthu ali yense wa kukhulupirira. Palibe ena amene ali ocimwa kwambiri kotero kuti sangathe kupeza mphamvu, kuyera mtima, ndi cilungamo mwa Yesu, amene anawafera. Iye ali kulindira kuwabvula zobvala zawo zodetsedwa ndi zoipa, ndi kuwabveka zobvala zoyera za cilungamo; Iye awauza kuti akhale ndi moyo, asafe.MOK 39.3

    Mulungu samaticitira ife monga amacitirana anthu. Maganizo ace ndi maganizo a cifundo, a cikondi ndi a cisomo. Iye ati, “Woipa asiye njira yace, ndi munthu wosalungama asiye maganizo ace, nabwere kwa Yehova; ndipo Yehova adzamcitira cifundo, ndi kwa Mulungu wathu, pakuti Iye adzakhululukira koposa.” “Ine ndafafaniza monga mtambo wocindikira zolakwa zako, ndi monga mtambo macimo ako.” (Yesaya 55: 7; 44: 22. )MOK 39.4

    “Pakuti sindikondwera nayo imfa ya wakufayo, ati Ambuye Yehova; cifukwa cace bwererani, nimukhale ndi moyo.” (Ezek. 18: 32. ) Satana ali wofulumira kuba citsimikizo codala ca Mulungu. Iye afuna kucotsa kaciyembekezo kali konse ndi kamuuni kali konse m’moyo; koma iwe usamulole kucita izi. Usamvere woyesayo, koma nena: “Yesu anafa kuti ine ndikhale ndi moyo. Iye andikonda ine, ndipo safuna kuti ndionongeke. Ndiri naye Atate wa kumwamba wa cifundo; ndipo ngakhale ndinanyoza cikondi cace, ngakhale ndinapeputsa madalitso ace, ndidzauka, ndipite kwa Atate wanga ndipo ndidzanena naye, ‘Ndinacimwira Kumwamba ndi pa maso panu, ndipo sindiri woyeneranso konse kuchulidwa mwana wanu: mundiyese ngati mmodzi wa anchito anu. ‘” Fanizoli likufotokozerani m’mene wosocera ati adzalandiridwire: “Pamene iye akali kutari, atate wace anamuona iye, ndipo anamva naye cifundo, nathamanga, nagwa pa khosi pace, namsomsonetsa iye.” (Luka 15: 18-20. )MOK 40.1

    Koma ngakhale fanizo limeneli, lomvetsa cisoni monga momwe lirimu, silingathe kufotokoza kokwana cifundo cosatha ca Atate wa kumwamba. Yehova anena mwa mneneri wace, “Ndakukonda iwe ndi cikondi cosatha: cifukwa cace ndakukoka iwe ndi kukukomera mtima.” (Yer. 31: 3. ) Wocimwa akali kutari ndi nyumba ya Atate, ali kungoononga cuma cace m’dziko la cilendo, mtima wa Atate uli kumdandaulira iye; ndipo cilakolako ciri conse m’moyo ca kubwerera kwa Mulungu, ndiwo madandaulo a Mzimu Woyera, kubwezera wocimwayo ku mtima wa cikondi wa Atate wace.MOK 40.2

    Ndi malonjezano olemera cotere a Baibulo patsogolo pako, kodi uli kukaikabe? Kodi uli kukhulupirira kuti pamene munthu wocimwa afuna kubwerera, nafuna kusiya zoipa zace, Yehova adzamkaniza iye kudza pa mapazi ace ali kulapa? Cotsa maganizo otero! Palibe kanthu kena kangapweteke mtima wako koposa kuganiza maganizo otere za Atate wathu wa kumwamba. Iye amadana ndi zoipa, koma amakonda wocimwa, ndipo anadzipereka yekha mwa Kristu, kuti onse amene afuna apulumutsidwe; nadzakhala nawo madalitso osatha mu ufumu wa ulemerero. Kodi akadanena cotani koposa m’mene adaneneramu pa kutsimikiza cikondi cace kwa ife? Iye ati, “Kodi mkazi angaiwale mwana wace wa pabere, kuti sangacitire cifundo mwana wombala iye? inde, awa angaiwale, koma ine sindingaiwale iwe.” (Yesaya 49: 15. )MOK 40.3

    Yang’anani kumwamba, inu amene muli kukaika ndi kunthunthumira; cifukwa Yesu ali ndi moyo kutipembedzera ife. Thokozani Mulungu cifukwa ca mphatso ya Mwana wace wokondedwa, ndi kupemphera kuti Iye asangokuferani kwacabe. Mzimu ali kukuitanani lero. Idzani ndi mtima wanu wonse kwa Yesu, ndipo mufunse madalitso ace.MOK 41.1

    Pamene muwerenga malonjezanowo, kumbukirani kuti ndiwo citsimikizo ca cikondi ndi cifundo cosaneneka. Mtima waukuru wa Cikondi Cosatha umakokedwa kwa wocimwa ndi cifundo cosatha. “Tiri ndi maomboledwe mwa mwazi wace, cikhululukiro ca zocimwa.” (Aefeso 1: 7. ) Inde, ingokhulupirani kuti Mulungu ndiye mthangati wanu. Iye afuna kubwezera cifanizo cace colungama mwa munthu. Pamene muyandikira cifupi ndi Iye, pakubvomereza ndi kulapa, adzayandikira kwa inu ndi cifundo ndi cikhululukiro.MOK 41.2

    Larger font
    Smaller font
    Copy
    Print
    Contents