Loading...
Larger font
Smaller font
Copy
Print
Contents
 • Results
 • Related
 • Featured
No results found for: "".
 • Weighted Relevancy
 • Content Sequence
 • Relevancy
 • Earliest First
 • Latest First
  Larger font
  Smaller font
  Copy
  Print
  Contents

  MUTU 7—YESO LA KUKHALA WOPHUNZIRA WA YESU

  “Ngati munthu ali yense ali mwa Kristu ali wolengedwa watsopano: zinthu zakale zapita, taonani, zakhala zatsopano.” (2 Akor. 5: 17. )MOK 43.1

  Kapena munthu sangadziwe nthawi yace kapena malo ace, kapena kulondola zonse m’nchito ya kutembenuka; koma zimenezi sizisonyeza kuti munthuyo sanatembenuke. Kristu anati kwa Nikodemo, “Mphepo iwomba pomwe ifuna, ndipo ukumva mau ace, koma sudziwa kumene icokera, ndi kumene imuka; cotero ali yense wobadwa mwa Mzimu.” (Yohane 3: 8. ) Monga mphepo imene iri yosaoneka, koma nchito zace zioneka bwino lomwe, coteronso Mzimu wa Mulungu pogwira nchito yace mu mtima wa munthu. Mphamvu ya kulenganso, imene sioneka ndi maso a munthu, imabala moyo watsopano mu mtima; imalenga munthu watsopano m’cifaniziro ca Mulungu. Ngakhale nchito ya Mzimu iri yacete ndi yosaoneka, nchito zace zimaonekera. Ngati mtima wakonzedwa ndi Mzimu wa Mulungu, makhalidwe a munthuyo adzacitira mboni. Ngakhale sitingathe kusintha mitima yathu, kapena kudziyanjanitsa tokha ndi Mulungu; ngakhale sitiyenera kudzikhulupirira tokha kapena nchito zathu zabwino, miyoyo idzaonetsera ngati cisomo ca Mulungu ciri mwa ife. Kusintha kudzaoneka m’makhalidwe ndi m’macitidwe athu. Kusiyana kudzaoneka bwino pakati pa zimene anali kucita ndi zimene ali kucita tsopano. Makhalidwe amaonekera, osati ndi nchito zabwino zocitika kamodzi kamodzi, kapenandi nchito zoipa zocitika kamodzi kamodzi, koma ndi mau olankhulidwa masiku onse ndi nchito za masiku onse.MOK 43.2

  Ndi zoonadi kuti munthu angathe kusonyeza makhalidwe abwino kunja kwace, wopanda mphamvu ya kulenganso ya Kristu. Kukonda citsanzo cabwino, ndi cifuniro ca kulemekeza ena zingampatse munthu makhalidwe olongosoka. Kudzicitira tokha ulemu kungatitsogolere ife kupewa maonekedwe a coipa. Mtima wa dyera ungathe kupatsa mofewa manja. Nanga tsono, tidzadziwa ndi ciani mwini wace wa mbali imene ife taima?MOK 43.3

  Ndani ali ndi mitima yathu? Maganizo athu ali ndi yani? Timakonda kulankhula za yani? Ndani watenga cikondi cathu copambana ndi nchito zathu zopambana? Ngati tiri a Kristu, maganizo athu adzakhala ndi Iye, tidzaganiza za Iye kopambana. Zonse zomwe tiri nazo ndi ife tomwe eni ace zidzaperekedwa kwa Iye. Tidzalakalaka kunyamula cifanizo cace, kupuma mzimu wace, kucita cifuniro cace, ndi kumkondweretsa Iye m’zinthu zonse.MOK 43.4

  Iwo amene asanduka olengedwa atsopano mwa Kristu Yesu adzabala zipatso za Mzimu, “Cikondi, cimwemwe, mtendere, kuleza mtima, cifundo, kukoma mtima, cikhulupiriro, cifatso, ciletso.” (Agalatiya 5: 22, 23. ) Sadzadzilinganizanso ndi zilakolako za kale, koma ndi cikhulupiriro ca Mwana wa Mulungu iwo adzatsata mapazi ace, adzaonetsera makhalidwe ace, nadziyeretsa okha monga Iyeyo ali woyera. Zinthu zomwe akadana nazo kale, azikonda tsopano; ndipo zomwe anali kukonda kale, adana nazo tsopano. Onyada ndi odzikuza amasanduka ofatsa ndi odzicepetsa mtima. Oledzera amasanduka odziletsa, Oipitsitsa amasanduka angwiro. Miyambo ndi mafano a dziko zasiyidwa. Akristu sadzafuna “kukometsera kwa kunja,” koma “munthu wobisika wa mtima, m’cobvala cosaola ca mzimu wofatsa ndi wacete.” (1 Pet. 3: 3, 4. )MOK 44.1

  Kulibe umboni wa kulapa ngati sikugwira nchito ya kukonzanso. Ngati wabweza cowinda cace, ngati wabweza comwe adaba, ngati wabvomereza zoipa zace, ndi kukonda Mulungu ndi anthu anzace, wocimwayo azindikire kuti wacokera ku imfa kulowa m’moyo.MOK 44.2

  Pamene ife, anthu ocimwa, tidza kwa Kristu, tikhala olandirana nawo cisomo cace cokhululukira, cikondi cimadzaza mu mtima. Katundu aliyense amapepuka; cifukwa gori la Kristu liri lofewa. Nchito imakhala cikondwererero nsembe nikhala yokondeweretsa. Njira imene kale inali kuoneka ya mdima, imasanduka yowala ndi dzuwa la cilungamo.MOK 44.3

  Cikondi ca makhalidwe a Kristu cidzaoneka mwa akuphunzira ace. Cinali cikondwerero cace kucita cifuniro ca Mulungu. Kukonda Mulungu, cangu ca ulemerero wace, ndizo zinali mphamvu yolamulira m’moyo mwa Mpulumutsi. Cikondi cinakometsa ndi kulemekeza nchito zace zonse. Cikondi ciri ca Mulungu. Mtima wosapatulidwa sungathe kucionetsera. Cimapezeka mu mtima m’ mene Yesu alamulamo. “Tikonda ife, cifukwa anayamba Iye kutikonda.” (1 Yohane 4: 19. ) Mu mtima umene unatsukidwa ndi cisomo ca Mulungu, cikondi ndilo tsinde la nchito. Cimakonza makhalidwe, cimalamulira maganizo, cimagonjetsa udani, ndi kukulitsa cikondano. Cikondi cimeneci cikakhala m’moyo, cimaukometsa, nicipereka cikoka cabwino ponse pozungulira.MOK 44.4

  Ziripo zoipa ziwiri zimene ayenera kuzipewa ana onse a Mulungu — makamaka iwo amene adza tsopano m’cisomo cace. Coyamba ndi comwe tafotokoza kale cija, ca kuyang’ana nchito zawo, kukhulupirira zomwe iwo angathe kucita, kudziyanjanitsa okha ndi Mulungu. Iye amene afuna kudziyeretsa yekha ndi nchito zace pa kusunga malamulo, ali kuyesa kucita cinthu cosatheka. Zonse zimene munthu angacite wopanda Kristu zimaonongeka ndi dyera ndi ucimo. Cingathe kutiyeretsa ife ndi cisomo ca Kristu cokha mwa cikhulupiriro.MOK 45.1

  Coipa caciwiri cosiyana, koma coopsanso, ndico cikhulupiriro ca kuti Kristu amamasula anthu kuti asamasunga malamulo a Mulungu; kuti popeza tidzalandira cisomo ca Kristu ndi cikhulupiriro cokha, nchito zathu ziribe kanthu ndi ciombolo cathu.MOK 45.2

  Koma zindikirani kuti kumvera si maonekedwe a kunja kokha, koma nchito ya cikondi. Malamulo a Mulungu ali citsimikizo ca makhalidwe ace; iwo ali citsimikizo ca cikondi cace, cifukwa cace ali maziko a ufumu wace m’mwamba ndi pa dziko lapansi. Ngati mitima yathu yakonzedwa m’cifaniziro ca Mulungu, ngati cikondi ca Mulungu, cadzalidwa mu mtima, kodi malamulo a Mulungu sadzacitika m’moyo mwace? Pamene maziko a cikondi adzalidwa mu mtima, pamene munthu akonzedwa monga mwa cifaniziro ca Iye amene anamlenga, lonjezano la cipangano catsopano likwanitsidwa “Ndidzapereka malamulo anga akhale pa mtima pawo, ndipo pa nzeru zawo ndidzawalemba.” (Heb. 10: 16. ) Ndipo ngati malamulo alembedwa mu mtima, kodi sadzakonza moyo? Kumvera — nchito za cikondi — ndico cizindikiro coona ca kukhala wakuphunzira wa Yesu. Motero malembo anena, “Cikondi ca Mulungu ndi ici, kuti tisunge malamulo ace.” Iye wakunena kuti, ndimdziwa Iye, koma wosasunga malamulo ace ali wabodza, ndipo mwa iye mulibe coonadi.” (1 Yohane 5: 3; 2: 4. ) M’malo mwa kummasula munthu kuti asamamvera, ndi cikhulupiriro cokha cimene cimatilandiritsa ife cisomo ca Kristu, cimene cimatithetsa ife kukhala omvera.MOK 45.3

  Sitimalandira cipulumutso cifukwa ca kumvera kwathu, cifukwa cipulumutso ndi mphatso yaulere ya Mulungu, yolandiridwa mwa cikhulupiriro. Koma kumvera ndico cipatso ca cikhulupiriro. “Ndipo mudiwa kuti Iyeyu anaonekera kudzacotsa macimo; ndipo mwa Iye mulibe cimo. Yense wakukhala mwa Iye sacimwa; yense wakucimwa sanamuona Iye, ndipo sanamdziwa Iye.” (1 Yohane 3: 5, 6. ) Nali yeso loona. Ngati tikhala mwa Kristu, ngati cikondi ca Mulungu cikhala mwa ife, maganizo athu, nchito zathu, zidzagwirizana ndi cifuniro ca Mulungu monga ciri kufotokozedwa m’malamulo ace oyera. “Tiana, munthu asasokeretse inu; iye wakucita colungama ali wolungama, monga Iyeyu ali wolungama.” (1 Yohane 3: 7. ) Cilungamo cifotokozedwa ndi mbendera ya malamulo oyera a Mulungu, ndiwo malamulo khumi operekedwa pa Sinai.MOK 45.4

  Cikhulupiriro ca mwa Kristu cimene anthu amanena kuti cimawamasula anthu kuti asamamvera Mulungu, si cikhulupiriro, koma ciyerekezo. “Pakuti muli opulumutsidwa ndi cisomo ca kucita mwa cikhulupiriro.” Koma “cikhulupiriro cikapanda kukhala nazo nchito cikhala cakufa m’kati mwacemo.” (Aefeso 2: 8; Yakobo 2: 17. ) Yesu anati za Iye yekha asanadze ku dziko lapansi. “Kucita cikondwero canu kundikonda, Mulungu wanga, ndipo malamulo anu ali m’kati mwa mtima mwanga.” (Salmo 40: 8. ) Ndipo asanakwerenso kumwamba Iye anati, “Monga Ine ndasunga malamulo a Atate wanga ndipo ndikhala m’cikondi ca. ce.” (Yohane 15: 10. ) Malembo ati, “Ndipo umo tizindikira kuti tamzindikira Iye, ngati tisunga malamulo ace.... Iye wakunena kuti akhala mwa Iye, ayeneranso mwini wace kuyenda monga anayenda Iyeyo.” (1 Yohane 2: 3-6. ) “Pakutinso Kristu anamva zowawa m’malo mwanu, nakusiyirani citsanzo kuti mukalondole mapazi ace.” (1 Pet. 2: 21. )MOK 46.1

  Makhalidwe a moyo wosatha ali cimodzimodzi tsopano monga anali masiku onse, —monga anali m’Paradaiso makolo athu oyamba asanacimwe, — omvera malamulo a Mulungu, cilungamo cangwiro. Ngati malandiridwe a moyo wosatha akadacepa kusiyana ndi awa, pompo cimwemwe ca maiko onse a kumwamba cikadakhala m’zoopsa. Njira ya ucimo ikadatseguka, pamodzi ndi tsoka ndi zisoni zace zonse zopanda malekezero.MOK 46.2

  Cinali cotheka kwa Adamu, asanagwe, kupanga makhalidwe olungama pa kumvera malamulo a Mulungu. Koma analephera kucita izi, ndipo cifukwa ca ucimo wace makhalidwe athu analephera, ndipo ife sitingathe kudzilungamitsa tokha. Popeza ndife ocimwa, osayera mtima, sitingathe kumvera malamulo oyera. Tiribe cilungamo ca ife eni coti tingathe kukwanitsa naco malamulo a Mulungu. Koma Kristu anatipangira ife njira yopulumukira. Iye anakhala pa dziko lapansi pakati pa mayeso onga timakomana nawo ife. Iye anakhala moyo wosacimwa. Iye anatifera ife, ndipo tsopano Iye afuna kutenga zoipa zathu ndi kutipatsa ife cilungamo cace. Ngati udzipereka kwa Iye, ndi kumlandira Iye ngati Mpulumutsi wako, pompo, ngakhale moyo wako uli woipa kwambiri, cifukwa ca Iye udzayesedwa wolu- ngama. Makhalidwe a Kristu aima m’malo mwa makhalidwe ako, ndipo ulandiridwa pamaso pa Mulungu ngati sunacimwa konse.MOK 46.3

  Koposa izi Kristu amasintha mtima. Amakhala mu mtima mwako mwa cikhulupiriro. Udzalumikizana ndi Kristu mwa cikhulupiriro ndi pa kupereka cifuniro cako kwa Iye kosalekeza; ndipo monga momwe ucita izi, adzacita mwa iwe kufuna ndi kucita komwe monga mwa cifuniro cace cokoma. Cotero mudzanena, “Moyo umene ndiri nawo tsopano m’thupi, ndiri nawo m’cikhulupiriro ca Mwana wa Mulungu, amene anandikonda ine, nadzipereka yekha cifukwa ca ine.” (Galatiya 2: 20. ) Yesu ananena cotere kwa ophunzira ace, “Pakuti wolankhula si ndinu, koma Mzimu wa Atate wanu akulankhula mwa inu.” (Mateyu 10: 20. ) Pompo, Kristu ali kugwira nchito mwa inu, mudzaonetsa mzimu umodzimodzi, mudzacita nchito zimodzimodzi. — nchito za cilungamo, za kumvera.MOK 47.1

  Conco tiribe kanthu mwa ife tokha kakudzitamandira. Palibe podzikuzira tokha. Ciyembekezo cathu ciri m’cilungamo ca Kristu cowerengedwa kwa ife, cocitika ndi Mzimu wace wakucita mwa ife.MOK 47.2

  Kulipo kusiyana kumene tiyenera kukumbukira pamene ife tilankhula za cikhulupiriro. Ciripo cikhulupiriro ca mtundu wina. Zakuti Mulungu alipo, ndi mphamvu, ndi coonadi ca mau ace, zimenezi ndi zoona zimene ngakhale Satana ndi amithenga ace sangathe kuzikana m’mitima yawo. Bible ati kuti “Ziwandanso zikhulupirira ndipo zinthunthumira.” (Yakobo 2: 19. ) Koma ici si cikhulupiriro.MOK 47.3

  Kumene si kuli cikhulupiriro congokhulupirira M’Mau ace okha, koma kupereka cifuniro kwa Iye; kumene mtima umaperekedwa kwa Iye, cikondi cimangirira pa Iye, kumeneko ndiko kuli cikhulupiriro, — cikhulupiriro cimene cimagwira nchito mwa cikondi, ndi kuyeretsa moyo. Ndi cikhulupiriro cimeneci mtima umakonzedwa m’cifaniziro ca Mulungu. Ndipo mtima umene m’makhalidwe ace osakonzedwa sugonja ku malamulo a Mulungu, pakuti ndithu sungathe kutero, tsopano umakondwera m’malamulo ace, nunena pamodzi ndi Davide, “Ha! Ndikondadi cilamulo canu; ndilingiriramo ine tsiku lonse.” (Salmo 119: 97. ) Ndipo cilungamo ca lamulo cikwanitsidwa mwa ife, “amene sitiyendayenda monga mwa thupi koma monga mwa Mzimu.” (Aroma 8: 4. )MOK 47.4

  Alipo ena amene adadziwa cikondi cokhululukira ca Kristu, ndi amene alakalakadi kukhala ana a Mulungu, koma nazindikira kuti makhalidwe awo sali angwiro, moyo wawo uli ndi zifukwa zambiri, ndipo ali ofulumira kukaika ngati kapena mitima yawo yakonzedwa ndi Mzimu Woyera kapena ai. Kwa oterewa ine ndinena, Musabwerere m’mbuyo ndi kulephera. Kawiri kawiri tidzigwada pansi ndi kulira pa mapazi a Yesu cifukwa cakupelewera kwathu ndi zolakwa zathu; koma tisagwe mphwayi. Ngakhale tagonjetsedwa ndi mdaniyo, sitinatayidwe ai, Mulungu sanatikane. Iai, Kristu ali pa dzinja la manja la Mulungu, amenenso amatipembedzera ife. Anatero Yohane wokondedwayo, “Zinthu izi ndakulemberani kuti musacimwe. Ndipo akacimwa wina Mnkhoswe tiri naye kwa Atate, ndiye Yesu Kristu wolungama.” (1 Yohane 2: 1. ) Ndipo musaiwale mau a Kristu, “Pakuti Atate yekha akonda inu.” (Yohane 16: 27. ) Iye afuna kukubwezerani kwa Iye yekha, kuti aone ungwiro ndi kuyera kwace kuli kuonekera mwa inu. Ndipo ngati mudzipereka nokha kwa Iye, Iye amene adayamba nchito yabwino mwa inu adzaicitabe kufikira tsiku la Yesu Kristu. Pempherani ndi mtima wonse; khulupirirani kolimba. Popeza sitikhulupirira mphamvu yathu, tiyeni tikhulupirire mphamvu ya Mombolo wathu, ndipo tidzamtamanda Iye amene ali thanzi la nkhope zathu.MOK 47.5

  Ngati udza cifupifupi ndi Yesu udzaoneka wocimwa kwambiri m’maso mwa iwe wekha; cifukwa masomphenya ako adzakhala angwiro, ndipo zonyansa zako zidzaoneka bwino lomwe polinganiza ndi makhalidwe ace angwiro. Umenewu ndi umboni kuti macenjerero a Satana ataya mphamvu yawo; ndi kuti cikoka ca mphamvu ya Mzimu wa Mulungu ciri kukudzutsa iwe.MOK 48.1

  Cikondi ca kuya ca Kristu sicingakhale mu mtima umene suzindikira zoipa zace. Moyo umene usinthidwa ndi cisomo ca Kristu, udzatamanda makhalidwe opatulika a umulungu wace; koma ngati sitiona zofooka zathu, ndiwo umboni wokwana kuti ife sitinaone ubwino ndi ukuru wa Kristu.MOK 48.2

  Ngati sitidzitamanda mwa ife tokha, tidzatamanda ungwiro ndi cikondi cosatha ca Mpulumutsi wathu. Tikaona zoipa zathu, tidzathamangira kwa Iye amene angathe kukhululukira; ndipo pamene moyo utazindikira kusowa mphamvu kwace, nufuna Kristu, adzadzionetsera yekha mu mphamvu. Tikazindikira kusowa kwathu tidzathamangira kwa Iye ndi ku Mau a Mulungu, ndipo tidzaona koposa makhalidwe ace, ndipo tidzaonetsera cifaniziro cace kokwana.MOK 48.3

  Larger font
  Smaller font
  Copy
  Print
  Contents