Loading...
Larger font
Smaller font
Copy
Print
Contents
 • Results
 • Related
 • Featured
No results found for: "".
 • Weighted Relevancy
 • Content Sequence
 • Relevancy
 • Earliest First
 • Latest First
  Larger font
  Smaller font
  Copy
  Print
  Contents

  MAU OYAMBA

  M’mapirikaniro ambiri mumamveka kuitana kwa mtengo wapatari, “Idzani kuno kwa Ine,”—kuitana kwa Mpulumutsi wacifundo amene mtima wace wa cikondi umapita kwa onse amene ali kusocera kulekana ndi Mulungu; ndipo m’mitima ya ambiri amene ali kulakalakadi cithangato ca kupeza Yesu, mumauka cifuniro ca kubwerera ku nyumba ya Atate. Oterewa kawiri kawiri amabwerezanso cifunso ca Tomasi, “Tidzadziwa njira bwanji?” Nyumba ya Atate iyang’anika ngati iri kutari, ndipo njira yace iwoneka yobvuta ndi yosadziwika. Nanga mapazi ace ngotani amene amatsogolera njira ya kunka kwathu?MOK 4.1

  Dzina la bukhuli lifotokoza nchito yace. Limasonyeza kwa Yesu kuti ndiye yekha angathe kukwanitsa zosowa za moyo, ndi kutsogolera mapazi okaika ndi otsimphina ku “njira ya mtendere.” Limatsogolera wofuna cilungamo ndi makhalidwe amphumphu, phazi limodzi limodzi m’njira ya moyo wa Cikristu, ku cidzalo ca dalitso cimene cimapezeka m’kudzipereka kotheratu ndi cikhulupiriro cosagwedezeka m’cisomo copulumutsa ndi mphamvu ya kusunga ya Bwenzi la ocimwa. Malangizo opezeka m’bukhu ili anatengera cisangalatso ndi ciyembekezo ku miyoyo yambiri yobvutika, ndipo lathangata otsata Yesu ambiri kuyenda molimbika ndi mokondwa m’mapazi a Mtsogoleri wawo wa kumwamba. Tiri kuyembekeza kuti lidzanyamula uthenga womwewu kwa enanso ambirimbiri amene ali kusowa cithangato comweci.MOK 4.2

  “Njira iwonekere Makwerero
  opita kumwamba.”
  MOK 4.3

  Zinali cotero ndi Yakobo, pamene, atapanikizidwa ndi mantha kuti chimo lace lamlekanitsa ndi Mulungu, iye anagona kupumula, ndipo “analota, ndipo taonani makwerero anaima pa dziko, ndipo pamwamba pace panafika kumwamba.” Motero cilumikizano ca kumwamba ndi dziko lapansi cinaululidwa kwa iye, ndipo mau a cisangalatso ndi ciyembekezo analankhulidwa kwa woyendayo ndi Iye amene anaima pamwamba pa makwererowo. Masomphenya a kumwambawa abwerezedwenso kwa ambiri pamene ali kuwerenga nthanoyi ya njira ya moyo.

  OSINDIKIZA.
  MOK 4.4

  Larger font
  Smaller font
  Copy
  Print
  Contents